Ndandanda ya Mlungu wa January 16
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 16
Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 18 ndime 19-23 ndi bokosi patsamba 191 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 34-37 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 35:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Yehova Ndi Woyenera Kumukhulupirira—Sal. 25:1-5 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tingayembekezere Kudzakhala Ndi Moyo Wosatha?—rs tsa. 292 ndime 7-9 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Zindikirani Maganizo a Wofunsayo. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 66, ndime 1 mpaka tsamba 68 ndime 3. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza m’bale kapena mlongo akufunsidwa funso. Wofalitsayo akulankhula yekha zimene wofunsayo angakhale akuganizira ndiponso kuda nazo nkhawa kenako akuyankha mogwira mtima.
Mph. 15: “Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero