Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Anzathu a Mboni za Yehova:
Ndife osangalala kwambiri kukulemberani kalata inu atumiki okhulupirika a Yehova, amene tsopano mukuposa 7 miliyoni. Mosakayikira, mukakumana ndi Mboni inzanu yochokera kudziko lakutali mumagwirizana nayo mosavutikira. (Yoh. 13:34, 35) Tikukhulupirira kuti mulimbikitsidwanso ndi nkhani zofotokoza chikhulupiriro ndiponso kupirira kwa abale ndi alongo anu amene akukhala m’mayiko osiyanasiyana ngati muli ndi mwayi wowerenga Yearbook ya 2012.
Malipoti ochokera padziko lonse akusonyeza kuti ambiri mwa inu mukuchitadi Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse. Amene muli ndi ana ang’onoang’ono mwagwiritsa ntchito luso lanu kuti muphunzitse ana anu. (Aef. 6:4) Mabanja akukondana kwambiri chifukwa cholimbikitsana mwauzimu pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. (Aef. 5:28-33) Kunena zoona, abale ndi alongo amene ali okha ndiponso a pa banja akupindula kwambiri ndi Kulambira kwa Pabanja kumene kukuwathandiza kuphunzira Mawu a Mulungu mozama.—Yos. 1:8, 9.
Tikudziwanso kuti ena mwa inu munatayikidwa katundu ndiponso okondedwa anu chifukwa cha masoka achilengedwe amene achitika posachedwapa. Tikuthokoza onse amene anadzipereka kukagwira ntchito yopereka chithandizo atamva za masokawa. (Mac. 11:28-30; Agal. 6:9, 10) Kuwonjezera pamenepa, m’mipingo muli abale enanso amene amathandiza abale awo amene akuvutika powapatsa zinthu zosiyanasiyana. Mofanana ndi Dorika, mukuchita “ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” (Mac. 9:36) Dziwani kuti Yehova akuona zimenezi ndipo adzakubwezerani.—Mat. 6:3, 4.
M’mayiko ena, ufulu wanu ukuponderezedwa ndi anthu amene amapotoza malamulo kuti ‘ayambitse mavuto.’ (Sal. 94:20-22) Yesu ananeneratu za chizunzo chimenechi. Chifukwa chodziwa zimenezi, mukupirira molimba mtima ndiponso kupitiriza kuthawira kwa Yehova. (Yoh. 15:19, 20) Dziwani kuti timakutchulani m’mapemphero athu nthawi zonse pamene mukupitiriza “kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.”—1 Pet. 3:13-15.
Tikukuthokozani nonsenu amene mukuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino chaka ndi chaka. Tikutero chifukwa Satana akuchita zonse zimene angathe mochenjera kwambiri pochititsa anthu kukhala ndi makhalidwe oipa. Pamene makhalidwe a anthu akuipiraipira, inuyo ‘mukupeza mphamvu kuchokera kwa Ambuye ndiponso kuchokera ku mphamvu zake zazikulu.’ (Aef. 6:10) Mukuvalanso “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu,” choncho mukutha ‘kulimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.’ (Aef. 6:11, 12) Dziwani kuti Yehova akugwiritsa ntchito chitsanzo chanu kuti ayankhe Satana amene amamutonza.—Miy. 27:11.
Ndife osangalala kudziwa kuti m’chaka cha 2011, pa mwambo wokumbukira imfa ya Ambuye wathu panafika anthu okwana 19,374,737. Zimenezi zinatheka chifukwa chakuti ambiri mwa inu munadzipereka kuchita upainiya wothandiza m’mwezi wa April mutamva kuti pakufunika apainiya ambiri. Anthu ambiri padziko lapansi anamva mawu otamanda Yehova kuchokera kwa Mboni zake zokhulupirika. (Aroma 10:18) Kaya munali nawo m’modzi wa anthu 2,657,377 amene anachita upainiya wothandiza mwezi wa April kapena munangowonjezera zochita, ife tinasangalala chifukwa cha mtima wanu wodzipereka ndiponso khama lanu.—Sal. 110:3; Akol. 3:23.
Chaka chatha, anthu atsopano okwana 263,131, anasonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova pobatizidwa. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha zimenezi ndiponso nonsenu chifukwa chogwira nafe ntchito youza ena kuti: “‘Bwera!’ Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” (Chiv. 22:17) Pa msonkhano wachigawo wa chaka cha 2011 tinamvera nkhani zosiyanasiyana zofotokoza Ufumu wa Mulungu umene unayamba kulamulira. Kuchokera nthawi imeneyi, tikunena motsimikiza kuposa kale kuti, “Ufumu wa Mulungu ubwere!” Chifukwa cholimbikitsidwa ndi mawu a Yesu akuti “ndikubwera mofulumira,” nafenso ndi mtima wonse tikugwirizana ndi mtumwi Yohane amene anayankha kuti “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.”—Chiv. 22:20.
Pamene mukupitiriza kukhala maso poyembekezera kuti ulosi umenewu ukwaniritsidwe, dziwani abale ndi alongo kuti timakukondani aliyense payekha. Pitirizani kusonyeza kuti mumakonda Yehova pa ‘zochita zanu.’—1 Yoh. 3:18.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova