Ndandanda ya Mlungu wa April 23
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 23
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 5 ndime 1-8 ndi bokosi patsamba 39 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 29-31 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 31:15-26 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mulungu Amafuna Kuti Akhristu Azisunga Sabata? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mariya Analidi Namwali pa Nthawi Imene Anabereka Yesu?—rs tsa. 255 ndime 3-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri fotokozani nkhani zochepa zimene zili m’magazini a mwezi wa May zimene zingakhale zothandiza m’gawo la mpingo wanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo, mungachitenso zimenezi ndi nkhani imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 25: “Chitani Khama pa Kuwerenga.” Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 21 ndime 1 mpaka tsamba 26 ndime 4. Pemphani m’bale kapena mlongo kuti afotokoze mmene amapezera nthawi yowerenga ndiponso mmene wapindulira. Limbikitsani onse kuti azipatula nthawi yophunzira Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo.
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero