Ndandanda ya Mlungu wa April 30
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 30
Nyimbo Na. 63 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 5 ndime 9-16 ndi bokosi patsamba 41 ndi 42 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 32-34 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa May.
Mph. 10: Mmene Mungayankhire Anthu Amene Amakana Kukambirana za Chipembedzo. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 91 ndime 3 mpaka tsamba 94 ndime 2. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zachidule.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 4:1-13, 18-20. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 5: “Timakobidi Tiwiri Tochepa Mphamvu.” Nkhani.
Nyimbo Na. 126 ndi Pemphero