Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/12 tsamba 2
  • Muzigwiritsa Ntchito Mwaluso ‘Lupanga la Mzimu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Mwaluso ‘Lupanga la Mzimu’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 5/12 tsamba 2

Muzigwiritsa Ntchito Mwaluso ‘Lupanga la Mzimu’

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito bwino “lupanga la mzimu”?

1 Kuti msilikali athe kugwiritsa ntchito zida zake bwinobwino kunkhondo, amafunika kuyamba waphunzira ndiponso kuzolowera kugwiritsa ntchito zidazo. N’chimodzimodzi ndi ifeyo pa nkhondo yathu yolimbana ndi Satana ndi gulu lake. Kuti tithe kugwiritsa ntchito bwinobwino “lupanga la mzimu,” tiyenera kuphunzira ndi kuzolowera kuligwiritsa ntchito. Mtumwi Paulo anati: “Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.”—2 Tim. 2:15.

2. Kodi tingatani kuti ‘tiziphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi’ mu utumiki?

2 Kodi tingatani kuti ‘tiziphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi’ mu utumiki? Sitingathe kuphunzitsa anthu momveka bwino zimene Baibulo limanena ngati ifeyo sitinamvetse mfundozo. Kuti timvetse bwino lemba la m’Baibulo, tiyenera kudziwa nkhani yonse kapena ndime imene muli lembalo. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kudziwa mavesi a kumbuyo ndi kutsogolo kwa vesilo.

3. Kodi tizikumbukira chiyani tikamafotokozera anthu malemba?

3 ‘Kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi’ sikutanthauza kungodziwa kufotokoza choonadi cha m’Malemba molondola ayi. Tisamaopseze anthu ndi Baibulo. Ngakhale kuti tingagwiritse ntchito Malemba poteteza choonadi ngati mmene Yesu anachitira poyesedwa ndi Mdyerekezi, Baibulo si chida chokakamizira anthu kuti angovomereza zimene tikunena. (Deut. 6:16; 8:3; 10:20; Mat. 4:4, 7, 10) Koma tiyenera kutsatira malangizo a mtumwi Petulo akuti: “Vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”—1 Pet. 3:15.

4. Kodi ndi “zinthu zozikika molimba” ziti zimene Mawu a Mulungu angathe kugwetsa? Perekani chitsanzo cha zochitika za kwanuko.

4 Kodi Mawu a Mulungu angachite zotani tikawagwiritsa ntchito moyenera? (Werengani 2 Akorinto 10:4, 5.) Choonadi cha m’Malemba chikhoza “kugwetsa zinthu zozikika molimba.” Izi zikutanthauza kuti Malemba akhoza kuthandiza munthu kuzindikira ziphunzitso zonama, makhalidwe oipa ndiponso nzeru za anthu zomwe ndi zolephera. Tingagwiritse ntchito Baibulo ngati lupanga lodulira maganizo aliwonse ‘otsutsana ndi kudziwa Mulungu.’ Zimene Baibulo limaphunzitsa zingathandize anthu kusintha maganizo awo, n’kuyamba kuganiza mogwirizana ndi choonadi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena