Ndandanda ya Mlungu wa May 28
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 28
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 6 ndime 17-24 ndi bokosi patsamba 48 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 49-50 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 49:28-39 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Dzina la Yehova Lili “Nsanja Yolimba”?—Miy. 18:10 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mariya Anapita Kumwamba ndi Thupi Lake Lenileni?—rs tsa. 258 ndime 2-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa June.
Mph. 25: “Inu Achinyamata, Khalani Ndi Mtima Wofuna Kutumikira Yehova.” Nkhani yokambirana. Funsani achinyamata awiri amene akuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Kodi n’chiyani chimene chinawathandiza kuti ayambe upainiya? Apindula chiyani chifukwa chochita upainiya? Ngati mumpingo wanu mulibe apainiya achinyamata, funsani atumiki othandiza awiri achinyamata. Kodi anali ndi maganizo otani asanakhale atumiki omwe anali olakwika? N’chiyani chimene chinawathandiza kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza? Tsindikani kuti achinyamata onse ayenera kutumikira Yehova akadali ana.
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero