Ndandanda ya Mlungu wa July 9
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 9
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 8 ndime 17-24 ndi bokosi patsamba 67 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 11–14 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 11:14-25 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Lemba la Yohane 6:53-57 Limatanthauza Chiyani?—rs tsa. 282 ndime 2-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kufatsa N’kutani, Nanga Khalidwe Limeneli Lingatilimbikitse Bwanji?—Zef. 2:3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Muzichita Maulendo Obwereza Mogwira Mtima. Nkhani yokambirana ndipo mugwiritse ntchito mafunso otsatirawa: (1) N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kukhala ndi cholinga tikamachita maulendo obwereza? (2) Kodi tizitenga nthawi yaitali bwanji pa maulendo obwereza oyambirira? (3) Kodi tiziyamba bwanji tikapita ku ulendo wobwereza? (4) Kodi tinganene chiyani ngati munthu wanena kuti sakufuna kuphunzira? (5) Tikamachita ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira kapepala, kabuku kapena magazini, kodi ndi nthawi iti imene tiyenera kumusonyeza buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo tingachite bwanji zimenezi? (6) Kodi tingatani kuti tithandize munthu yemwe sakupezekanso panyumba kuti apitirizebe kukhala ndi chidwi chophunzira Mawu a Mulungu? (7) Tikamachita maulendo obwereza, kodi tingatani kuti tithandize ofalitsa amene sanazolowere kulalikira?
Mph. 15: “Kodi Muli Ndi ‘Chifukwa Chosangalalira’?” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime yachinayi, limbikitsani onse kuti azipereka malipoti a utumiki wakumunda. Kambiranani mfundo zimene zingakhale zothandiza kuchokera m’buku la Gulu, tsamba 88 mpaka 90.
Nyimbo Na. 9 ndi Pemphero