Ndandanda ya Mlungu wa November 19
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 19
Nyimbo Na. 53 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 15 ndime 8-12 ndi bokosi patsamba 118 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Obadiya 1 mpaka Yona chaputala 4 (Mph. 10)
Na. 1: Yona 2:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kulambira Koona Kumathandiza Bwanji Kuti Anthu Amitundu Yonse Akhale Ogwirizana?—Sal. 133:1 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani “Paradaiso” Wotchulidwa pa Luka 23:43 Sangakhale Mbali Ina ya Hade Kapena ya Kumwamba?—rs tsa. 337 ndime 1–tsa. 338 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph 15: Kutumikira Kudera Kumene Kukufunika Antchito Ambiri Kumabweretsa Madalitso Ambiri Ochokera kwa Yehova. Nkhani yokambirana yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011, tsamba 4 mpaka 6. Pemphani omvera kuti anene zimene tikuphunzirapo.
Mph 15: “Musafulumire Kuganiza Kuti Simungakwanitse—Zimene Mungachite Ngati Mumachita Mantha.” Mafunso ndi mayankho. Mwachidule funsani wofalitsa amene sanaphunzire mokwanira sukulu kapena amene ndi wamanyazi koma amagwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo.
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero