Ndandanda ya Mlungu wa January 14
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 14
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 17 ndime 15-19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu 7-11 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 10:24-42 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Muzichita Zinthu Mwanzeru Ndipo Muzipewa Zinthu Zopanda Pake—1 Sam. 12:21; Miy. 23:4, 5 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Zinthu Ziti Zimene Tiyenera Kutchula Tikamapemphera?—rs tsa. 341 ndime 8–tsa. 342 ndime 6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Athandizeni pa Zosowa Zawo. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 188, ndime 4 mpaka tsamba 189, ndime 4. Funsani mwachidule munthu amene anapita patsogolo chifukwa chakuti anthu ena anamusonyeza chidwi.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 4:1-11. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Mph. 10: “Perekani Umboni Mokwanira.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero