Ndandanda ya Mlungu wa April 15
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 15
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 21 ndime 14-22 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Luka 13-17 (Mph.10)
Na. 1: Luka 16:16-31 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mulungu Amationa Kuti Ndife Osafunika Chifukwa Chakuti Ndife Opanda Ungwiro?—Sal. 103:8, 9, 14; Agal. 6:9 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Anthu Onse Ndi Ana a Mulungu?—rs tsa. 237 ndime 2-6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani Yokambirana.
Mph. 10: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Gawo 2. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 112, ndime 3 mpaka tsamba 114, ndime 1. Funsani mpainiya mmodzi kapena awiri kuti afotokoze zimene asintha pa moyo wawo kuti akwanitse kuchita upainiya.
Mph. 10: Kodi Mumalalikira Kuntchito Kwanu? Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso awa: (1) N’chifukwa chiyani nthawi zonse ndi bwino kuti anthu amene mumagwira nawo ntchito azidziwa kuti ndinu wa Mboni za Yehova? (2) Kodi mungawadziwitse bwanji? (3) Kodi kuntchito kungachitike zinthu zotani zomwe zingatipatse mwayi wolalikira? (4) N’chifukwa chiyani ndi bwino kuti ngati n’zotheka tizikhala ndi Baibulo komanso mabuku athu ena kuntchito? (5) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kulalikira munthu kwa nthawi yaitali pa nthawi yomwe tikufunika kugwira ntchito? (6) Kodi ndi zinthu zosangalatsa zotani zimene zinakuchitikirani pamene mumalalikira kuntchito?
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero