Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 29, 2013. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi Yesu anakumbutsa omvera ake mfundo yofunika kwambiri iti yokhudza ukwati, yomwe yatchulidwa pa Maliko 10:6-9? [Mar. 4, w08 2/15 tsa. 30 ndime 8]
2. Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza chiyani? (Maliko 12:30) [Mar. 4, w97 10/15 tsa. 13 ndime 4]
3. Kodi mawu akuti “masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka” otchulidwa pa Maliko 13:8 akutanthauza chiyani? [Mar. 11, w08 3/15 tsa. 12 ndime 2]
4. Kodi Luka anafufuza kuti pamene ankalemba buku lake la Uthenga Wabwino? (Luka 1:3) [Mar. 18, w09 3/15 tsa. 32 ndime 3]
5. Kodi mfundo yakuti Satana amafunafuna “nthawi ina yabwino” kuti atiyese ngati tili okhulupirika, iyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? (Luka 4:13) [Mar. 25, w11 1/15 tsa. 23 ndime 10]
6. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mawu a pa Luka 6: 27, 28? [Mar. 25, w08 5/15 tsa. 8 ndime 4]
7. Popeza kuti Yesu anali asanafe monga nsembe ya dipo, zinatheka bwanji kuti akhululukire mayi amene ankadziwika monga wochimwa? (Luka 7: 37, 48) [Apr. 1, w10 8/15 tsa. 6-7]
8. Kodi otsatira a Khristu ‘amadana’ ndi achibale awo m’njira yotani? (Luka 14:26) [Apr. 15, w08 3/15 tsa. 32 ndime 1; w92 7/15 tsa. 9 ndime 3-5]
9. Kodi zizindikiro zomwe zidzakhale “padzuwa, mwezi ndi nyenyezi” zidzakhudza bwanji anthu? (Luka 21:25) [Apr. 22, w97 4/1 tsa. 15 ndime 8-9]
10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani ya mmene tiyenera kupempherera tikakumana ndi mavuto aakulu? (Luka 22:44) [Apr. 29, w07 8/1 tsa. 6 ndime 2]