Ndandanda ya Mlungu wa April 29
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 29
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 22 ndime 7-14 ndi bokosi patsamba 174 ndi 177 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Luka 22-24 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyambirira m’mwezi wa May. Limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Kambirananinso nkhani yakuti: “Kodi Nthawi Zonse Mumaona Zimene Zili pa Bolodi la Chidziwitso?”
Mph. 10: Uthenga Umene Tiyenera Kulalikira ndi Wakuti, “Uthenga Uwu Wabwino wa Ufumu.” Nkhani yolimbikitsa yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki patsamba 279 mpaka 281.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 16:21-23 ndi Luka 9:22-26. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero