Ndandanda ya Mlungu wa April 22
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 22
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 22 ndime 1-6 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Luka 18-21 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 18:18-34 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Zidzathekadi Kuti Anthu a Mitundu Yonse Adzagwirizane Monga Abale ndi Alongo?—rs tsa. 238 ndime 1-tsa. 239 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kufatsa N’kutani, N’chifukwa Chiyani Khalidwe Limeneli Lili Lofunika Ndipo Tingatani Kuti Tikhale Nalo?—Zef. 2:2, 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Tizivala ndi Kudzisamalira Moyenera. Kukambirana kwa mafunso ndi mayankho kuchokera m’nkhani yomwe ili m’buku la Chikondi cha Mulungu patsamba 56 ndi 57, ndime 11 mpaka 15. Limbikitsani abale ndi alongo kuti azivala mwaulemu pa zochitika zonse zachikhristu monga paukwati, pamaliro, mu utumiki komanso ku misonkhano yachikhristu ku Nyumba ya Ufumu.
Mph. 15: “Thandizani Ena Kuti Ayenerere Maudindo.” Nkhani yolimbikitsa yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2011 patsamba 28 mpaka 32. Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Pemphani mkulu kapena mtumiki wothandiza kuti afotokoze zimene anthu ena anachita pomuthandiza kuti ayenerere udindo womwe ali nawo. Limbikitsani abale onse obatizidwa kuti aganizire zimene angachite kuti atumikire anthu ena pa maudindo osiyanasiyana.
Nyimbo Na. 121 ndi Pemphero