Ndandanda ya Mlungu wa May 27
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 27
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 23 ndime 16-19 ndi bokosi patsamba 188 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yohane 12-16 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 12:20-36 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Nsembe ya Yesu Inagwira Ntchito Choyamba kwa Ndani, Ndipo Cholinga Chake Chinali Chotani?—rs tsa. 124 ndime 2-3 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani M’pomveka Kunena Kuti Yehova Ndi “Mulungu Amene Amapatsa Mtendere”?—Aroma 15:33 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani. Pogwiritsa ntchito kuseri kwa Nsanja ya Olonda, sonyezani mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyambirira m’mwezi wa June. Limbikitsani ofalitsa onse kuti ayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: Kuthirira Mbewu Zimene Timabzala. (1 Akor. 3:6-9) Nkhani yokambirana pogwiritsira ntchito mafunso awa: (1) Kodi chimakusangalatsani n’chiyani pochita ulendo wobwereza? (2) N’chifukwa chiyani ofalitsa ena amaona kuti kuchita ulendo wobwereza ndi kovuta? (3) Kodi mavuto amenewa angathetsedwe bwanji? (4) Kodi tingathandizidwe bwanji ngati timaona kuti kuchita ulendo wobwereza ndi kovuta? (5) Kodi mumatani kuti musamaiwale munthu amene anasonyeza chidwi komanso kukumbukira mfundo imene munakambirana, buku limene munamugawira ndiponso zinthu zina? (6) Kodi mumakonzekera bwanji maulendo obwereza? (7) N’chifukwa chiyani mlungu uliwonse tiyenera kukonza nthawi yopitanso kwa anthu amene anasonyeza chidwi?
Mph. 10: “Muzigwiritsira Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa.” Nkhani yokambirana. Pemphani abale ndi alongo kuti afotokoze mmene anapindulira ndi mavidiyo athu asanakhale a Mboni.
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero