Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Chaka chatha, pa msonkhano wapadera umene unachitika m’dera la C-11, munthu wina wazaka 89 anabatizidwa. Iye kwa zaka zambiri anali mfumu, komanso ankakonda gulewamkulu asanakhale wa Mboni. Iye atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni, anasiya zinthu zonsezi ndipo tsopano ndi m’bale wathu. Tiyeni tonse tipitirize kuthandiza “anthu a mtundu uliwonse” kuti adziwe Yehova.—1 Tim. 4:10.