Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa June
“Pafupifupi munthu aliyense amene timalankhula naye amafuna kuti padzikoli pakhale mtendere. Koma nkhondo zikuchitikabe. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho?” [Yembekezani ayankhe.] Kenako muonetseni kuseri kwa Nsanja ya Olonda ya June 1. Kambiranani mfundo zimene zili pa funso loyamba ndipo kenako werengani lemba limodzi limene likupezeka pansi pa funso limeneli. Mugawireni magaziniwo, ndipo muuzeni kuti mudzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Dziwani izi: Muyenera kuchita chitsanzo chimenechi pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda wa pa June 1.
Nsanja ya Olonda June 1
“Tikulankhula ndi anthu mwachidule za vuto limene lili ponseponse. Anthu ambiri akumanapo ndi vuto la tsankho pa moyo wawo. Kodi mukuganiza kuti pali dziko lina limene kulibe tsankho? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mmene Yehova amaonera anthu onse. [Werengani Machitidwe 10:34.] Magazini awa akufotokoza zimene Mulungu adzachite kuti athetseretu tsankho.”
Galamukani! June
“Aliyense padziko lapansili amafuna kukhala ndi moyo wabwino. Koma kodi mukuganiza kuti tingathe kukhala ndi moyo wabwino ngati titagula zinthu zambirimbiri? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mfundo yochititsa chidwi iyi imene Yesu ananena. [Werengani Luka 12:15.] Magazini awa akufotokoza mmene tiyenera kuonera chuma komanso mmene tingagwiritsire ntchito ndalama zathu mwanzeru.”