Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May ndi June: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo, kapena Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. July and August: Gawirani kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena timabuku takuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
◼ Tikulimbikitsa akulu onse kuti ayenera kumatumiza lipoti la utumiki wakumunda la mpingo pogwiritsa ntchito njira ya SMS pa foni ya m’manja kapena Intaneti pa Webusaiti yathu ya jw.org. Ngati simungathe kutumiza lipoti la utumiki wakumunda pogwiritsira ntchito Intaneti pa Webusaiti yathu ya jw.org kapena polemba SMS pa foni, mungapitirize kutumiza malipotiwa kudzera pa fomu ya S-1.