Ndandanda ya Mlungu wa June 3
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 3
Nyimbo Na. 43 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 24 ndime 1-9 ndi bokosi patsamba 193 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yohane 17-21 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 21:15-25 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Sitiyenera ‘Kutsatira Khamu’?—Eks. 23:2; Miy. 1:10 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndani Amenenso Akupindula ndi Nsembe ya Yesu?—rs tsa. 125 ndime 1-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa June. Nkhani yokambirana. Pa nthawi yosapitirira mphindi imodzi, fotokozani nkhani zochepa za m’magaziniwo zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze funso lokopa chidwi limene angafunse. Apempheninso kutchula lemba limene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi Galamukani! Ndipo ngati nthawi ilipo mungachite zomwezo ndi nkhani ina imodzi ya m’magaziniwa. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: N’chifukwa Chiyani Timapereka Malipoti a Utumiki Wakumunda? Nkhani yokambidwa ndi mlembi yochokera m’buku la Gulu, tsamba 88 ndime 1 mpaka tsamba 90 ndime 1.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero