Dipo
Tanthauzo: Mtengo wolipiridwa kuwombolera kapena kumasula kungongole kapena mkhalidwe wopsinjika. Mtengo wa dipo wapadera koposa ndiwo wa mwazi wokhetsedwa wa Yesu Kristu. Mwa kulipirira mtengo wa dipo limenelo kumwamba, Yesu anatsegulira njira ana a Adamu yolanditsidwira ku uchimo ndi imfa zimene tonsefe timalandira monga choloŵa chifukwa cha uchimo wa kholo lathu Adamu.
Kodi ndimotani mmene imfa ya Yesu Kristu inaliri yosiyana ndi ya ena amene afikira kukhala ophedwera chikhulupiriro?
Yesu anali munthu wangwiro. Anabadwa ali wopanda banga lirilonse lauchimo ndipo anasunga ungwiro umenewo mpaka imfa yake. “Sanachita tchimo.” Iye anali “wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa.”—1 Pet. 2:22; Aheb. 7:26.
Iye anali Mwana wapadera wa Mulungu. Mulungu mwini anachitira umboni za ichi momvekera kuchokera kumwamba. (Mat. 3:17; 17:5) Mwana ameneyu anali atakhala ndi moyo kalero kumwamba; kupyolera mwa iye Mulungu anachititsa anthu ena onse ndi zinthu zonse m’chilengedwe chonse kukhalako. Kuti akwaniritse chifuniro Chake, Mulungu anafunikira kusamutsira mwanjira yozizwitsa moyo wa Mwana ameneyu kumimba ya namwali kotero kuti abadwe kukhala munthu. Kugogomezera kuti iye anali atakhala munthu, Yesu analankhula za iyemwini monga Mwana wamunthu.—Akol. 1:15-20; Yoh. 1:14; Luka 5:24.
Iye sanali wopanda mphamvu pamaso pa akumupha. Iye anati: “Nditaya ine moyo wanga . . . Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya ine ndekha.” (Yoh. 10:17, 18) Iye anakana kupempha makamu a angelo kuloŵeramo kumthandiza. (Mat. 26:53, 54) Ngakhale kuli kwakuti anthu oipa anali kuloledwa kukwaniritsa zolinganiza zawo m’kumupha, imfa yake inalidi ya nsembe.
Mwazi wake wokhetsedwa uli ndi mtengo wopereka chilanditso kwa ena. “Mwana wamunthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.” (Marko 10:45) Motero imfa yake inali kwakukulukulu kuphedwera chikhulupiriro chifukwa cha kukana kuleka zikhulupiriro zake.
Wonaninso tsamba 70, 71, pamutu wakuti “Chikumbutso.”
Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kuti dipo liperekedwe mwadongosolo limene linaperekedwera kuti ife tikhale nawo moyo wamuyaya?
Aroma 5:12: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse chifukwa kuti onse anachimwa.” (Mosasamala kanthu za mmene tingakhalire moyo mwachilungamo, tonsefe tiri ochimwa mwachibadwa. [Sal. 51:5] Palibe njira imene tingapezere kuyenera kwa kukhala ndi moyo kosatha.)
Aroma 6:23: “Mphotho yake ya uchimo ndiimfa.”
Sal. 49:6-9: “Iwo akutama kulemera kwawo; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chawo; kuwombola mbale sangadzamuwombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu; (popeza chiwombolo cha moyo wawo nchamtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthaŵi zonse:) kuti akhale ndi moyo osafa, osawona chivundi.” (Palibe munthu wopanda ungwiro amene angapereke njira ya kuwombolera munthu wina kuuchimo ndi imfa. Ndalama zake sizingagule moyo wamuyaya, ndipo moyo wake kuikidwa mu imfa, kukhala malipiro amene ndiiko komwe adzadza chifukwa cha uchimo, alibe mtengo kulinga ku kuwombola aliyense.)
Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanangolamula kuti, ngakhale ngati Adamu ndi Hava ayenera kufa kaamba ka chipanduko chawo, ana awo onse amene akamvera Mulungu akakhala ndi moyo kosatha?
Chifukwa chakuti Yehova ali “wa kukonda chilungamo ndi chiŵeruzo.” (Sal. 33:5; Deut. 32:4; Yer. 9:24) Motero, njira imene anasamalira nayo mkhalidwewo inachirikiza chilungamo chake, nifikitsa zofunika za chiŵeruzo cholungama kotheratu, ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, inasonyeza kukula kwa chikondi chake ndi chifundo. Kodi ziri choncho motani?
(1) Adamu ndi Hava anali asanabale ana asanachimwe, chotero palibe amene anabadwa angwiro. Mbadwa zonse za Adamu zinabadwira mu uchimo, ndipo uchimo umatsogolera ku imfa. Ngati Yehova akanangonyalanyaza ichi, kutero kukanakhala kulandula miyezo ya iyemwini yolungama. Mulungu sakanachita zimenezo ndipo mwa kutero kukhala ndi mbali ya chisalungamocho. Iye sananyalanyaze zofunika za chiŵeruzo chotheratu; chotero palibe cholengedwa chaluntha chimene mwalamulo chikanapeza liwongo pamfundoyi.—Aroma 3:21-26.
(2) Popanda kunyalanyaza zofunika za chiŵeruzo cholungama, kodi ndimotani mmene makonzedwe akanapangidwira a kuwombola ana a Adamuwo amene akanasonyeza kumvera kwachikondi kwa Yehova? Ngati munthu wangwiro anali kudzafa monga nsembe, chiŵeruzo cholungama chikanachititsa kuti moyo wangwiro uperekedwe kukwirira machimo a awo amene mwachikhulupiriro akanavomereza kakonzedweko. Popeza tchimo lamunthu mmodzi (la Adamu) linali ndi thayo la kuchititsa banja lonse laumunthu kukhala lochimwa, mwazi wokhetsedwa wa munthu wina wangwiro (kwenikweni, Adamu wachiŵiri), pokhala wamtengo wolinganira, ukanaliganiza miyezo ya chiŵeruzo cholungama. Chifukwa chakuti Adamu anali wochimwa dala, sakanakhoza kupindula; koma chifukwa chakuti chilango chimene anthu onse anali oyenerera kulipirira kaamba ka uchimo chikalipiriridwa mwanjirayi ndi munthu wina, mbadwa za Adamu zikakhoza kulanditsidwa. Koma panalibe munthu wangwiro wotero. Anthu sakanakhoza kukwaniritsa konse zofunika zimenezo za chiŵeruzo chotheratu. Chotero, monga chisonyezero cha chikondi chachikulu mwa kutayikiridwa kwakukulu iyemwini, Yehova mwiniyo anapanga makonzedwewo. (1 Akor. 15:45; 1 Tim. 2:5, 6; Yoh. 3:16; Aroma 5:8) Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anali wofunitsitsa kuchita mbali yake. Modzichepetsa anasiya ulemerero wake wakumwamba ndi kukhala munthu wangwiro, Yesu anafera anthu.—Afil. 2:7, 8.
Fanizo: Mutu wabanja ungafikire kukhala mpandu ndi kuŵeruziridwa ku imfa. Ana ake angasiyidwe mu mkhalidwe wa aumphaŵi ndi mkhalidwe wa ngongole wopanda chiyembekezo. Mwinamwake mwachikondi agogo ŵawo aloŵerera mmalo mwawo, akumapanga makonzedwe kupyolera mwa mwana amene akukhala nawo kulipirira ngongole zawo ndi kuwatsegulira njira ya kuthekera kwa moyo watsopano. Ndithudi, kuti apindule, anawo ayenera kuvomereza kakonzedweko, ndipo agogowo mwanzeru angafune zinthu zina monga chitsimikiziro chakuti anawo sadzatsanzira njira ya atate ŵawo.
Kodi nkwayani kumene mtengo wa nsembe ya Yesu unagwirako ntchito choyamba, ndipo ncholinga chotani?
Aroma 1:16: “Uthenga Wabwino [wonena za Yesu Kristu ndi mbali yake m’chifuno cha Yehova] . . . uli mphamvu ya Mulungu ya kupulumutsa munthu aliyense wa kukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.” (Chiitano cha kupindula ndi kakonzedwe ka chipulumutso kupyolera mwa Kristu chinaperekedwa choyamba kwa Ayuda, ndiyeno kwa osakhala Ayuda.)
Aef. 1:11-14, NW: “M’chigwirizano ndi [Kristu] ife [Ayuda, kuphatikizapo mtumwi Paulo] tinagaŵiridwanso kukhala oloŵa nyumba [Oloŵa nyumba a chiyani? A Ufumu wakumawamba] . . . kuti tiyenera kutumikira kaamba ka chitamando cha ulemerero wake, ife amene takhala oyamba kuyembekezera mwa Kristu. Koma inunso [Akristu otengedwa kumitundu ya Akunja, monga momwe analiri ochuluka m’Efeso] munayembekezera mwa iye pambuyo pakumva mawu a chowonadi, mbiri yabwino yonena za chipulumutso chanu. Koma mwa iyenso, pambuyo pa kukhulupirira kwanu, munasindikizidwa ndi mzimu woyera wolonjezedwawo, umene uli chizindikiro chapasadakhale cha choloŵa chathu, kaamba ka chifuno cha kumasulidwa ndi dipo kukhala chuma cha Mulungu mwini, ku ulemerero wake.” (Choloŵa chimenecho, monga momwe chasonyezedwera pa 1 Petro 1:4, chasungidwira kumwamba. Chivumbulutso 14:1-4 chimasonyeza kuti awo amene amatengamo mbali ali ndi chiŵerengero cha 144 000. Limodzi ndi Kristu, amenewa adzatumikira monga mafumu ndi ansembe pa anthu kwazaka 1 000, m’nthaŵi imene chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi kukhala paradaiso wokhalidwa ndi mbadwa zangwiro za anthu oyamba chidzakwaniritsidwa.)
Kodi ndani amenenso akupindula m’tsiku lathu ndi nsembe ya Yesu?
1 Yoh. 2:2: “Iye [Yesu Kristu] ndiye chiwombolo cha machimo athu [aja a mtumwi Yohane ndi a Akristu ena odzozedwa ndi mzimu], komanso a dziko lonse lapansi [ena a mtundu wa anthu, amene mwanjirayo chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi chikuchititsidwa kukhala chothekera].”
Yoh. 10:16: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (“Nkhosa zina” zimenezi zimaloŵa pansi pa chisamaliro chachikondi cha Yesu Kristu pamene otsalira a “kagulu kankhosa” ka oloŵa nyumba a Ufumu akali chikhalibe padziko lapansi; motero “nkhosa zina zingagwirizanitsidwe ndi oloŵa nyumba a Ufumu kukhala mbali ya “gulu limodzi.” Iwo onse amasangalala ndi madalitso ochuluka ofanana kuchokera mu nsembe ya Yesu koma samatero mofanana ndendende, chifukwa chakuti ali ndi zoikidwiratu zosiyana.)
Chiv. 7:9, 14, NW: “Zitatha zinthu izi ndinawona, ndipo tawonani! Khamu lalikulu limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lochokera m’mitundu yonse ndi mafuko ndi manenedwe . . . amenewa ndiwo anthu amene akutuluka m’chisautso chachikulu, ndipo iwo achapa miinjiro yawo naiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” (Chotero, mamembala a khamu lalikulu akukhala ndi moyo pamene chisautso chachikulu chiyamba, ndipo ali ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu chifukwa cha kusonyeza chikhulupiriro m’dipo. Chilungamo chimene amanenedwa kukhala anali nacho chifukwa cha ichi nchokwanira kwa iwo kuwatetezera ali moyo padziko lapansi kupyola chisautso chachikulu.)
Kodi padzakhala kusangalala ndi madalitso amtsogolo otani chifukwa cha dipo?
Chiv. 5:9, 10: “Aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, [Mwanawankhosa, Yesu Kristu] Muyenera kulandira bukhulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.” (Dipo linali chinthu chofunika m’kutsegulira njira kumoyo wakumwamba kaamba ka awo amene adzalamulira ndi Kristu. Mwamsanga olamulira onse m’boma latsopano la dziko lapansi adzakhala pamipando yawo yachifumu kumwamba.)
Chiv. 7:9, 10, NW: “Tawonani! Khamu lalikulu limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lochokera m’mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, lirinkuimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa [Yesu Kristu, amene anafa monga mwana wankhosa wansembe], lovala miinjiro yoyera; ndipo m’manja mwawo munali makhwatha akanjedza. Ndipo amafuula ndi mawu aakulu, kumati: ‘Chipulumutso tichipeza kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu ndi kwa Mwanawankhosa.’” (Chikhulupiriro mu nsembe ya Kristu ndicho chinthu chachikulu m’kupulumutsidwa kwa khamu lalikulu iri kupyola chisautso chachikulu.)
Chiv. 22:1, 2: “Anandiwonetsa mtsinje wa madzi amoyo, wonyezimira ngati krustalo, wotuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Pakhwalala lake, ndi tsidya iri lamtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wa kubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” (Motero, kugwiritsidwa ntchito kwa mtengo wa nsembe ya Mwanawankhosa wa Mulungu, Yesu Kristu, mbali yofunika ya makonzedwe opangidwa ndi Mulungu kuchiritsira anthu ziyambukiro zonse za uchimo ndi kuwakhozetsa kukhala ndi moyo wamuyaya.)
Aroma 8:21, NW: “Chilengedwe chenichenicho [anthu] chidzamasulidwanso kuukapolo wa chivundi ndi kukhala ndi ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”
Kodi timafunikira kuchitanji kuti tipindule kosatha ndi nsembe yangwiro ya Yesu
Yoh. 3:36: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzawona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”
Aheb. 5:9: “Ndipo pamene [Yesu Kristu] anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”
Kodi nchiyani chimene makonzedwe a dipo amavumbula ponena za mmene Mulungu amalingalirira za mtundu wa anthu?
1 Yoh. 4:9, 10: “Umo chidawoneka chikondi cha Mulungu kwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.”
Aroma 5:7, 8, NW: “Pakuti munthu aliyense sadzamfera munthu wolungama; ndithudi, kaamba ka munthu wabwino, mwinamwake, samalimbikadi mtima kumfera. Koma Mulungu amasonyeza chikondi chake cha iyemwini kwa ife m’chakuti, pamene ife tinali chikhalibe ochimwa, Kristu anatifera.”
Kodi nchiyambukiro chotani chimene makonzedwe amenewa ayenera kukhala nacho ponena za mmene timagwiritsirira ntchito miyoyo yathu?
1 Pet. 2:24, NW: “Iye mwini ananyamula machimo athu m’thupi lake iyemwini pamtengo, mmalo mwakuti ife tikafafaniziridwe machimo ndi kukhala ndi moyo m’chilungamo.” (Kaamba ka zonse zimene Yehova ndi Mwana wake wachita kutiyeretsa ku uchimo, tiyenera kuyesayesa mwaphamphu kugonjetsa zikhoterero za uchimo. Kuyenera kukhala kosalingalirika kotheratu kuti ife mwadala tichite kanthu kalikonse kamene tidziŵa kuti nkuchimwa!)
Tito 2:13, 14: “Yesu Kristu . . . anadzipereka yekha mmalo mwa ife kuti akatiwombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pantchito zokoma.” (Chiyamikiro kaamba ka makonzedwe odabwitsa awa chiyenera kutisonkhezera kukhala ndi mbali mwachangu m’ntchito zimenezo zimene Kristu anagaŵira kwa otsatira ake owona.)
2 Akor. 5:14, 15: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma iye amene adawafera iwo, nauka.”