Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
“Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—YOHANE 3:16.
1, 2. Fotokozani chothetsa nzeru chimene mtundu wa anthu wakhala nacho.
TAYEREKEZERANI kuti mukudwala nthenda imene mosakayika itha kukuphani pokhapo mutachitidwa opaleshoni. Kodi mungamve bwanji ngati mtengo wa opaleshoni imeneyo simungaukwanitse mpang’ono pomwe? Bwanji ngati ngakhale ndalama zimene banja lanu lasonkhanitsa kuwonjezeraponso za anzanu sizikukwanira? Kukhala ndi chothetsa nzeru choika moyo pachiswe ngati chimenechi kungakhale kokhumudwitsa zedi!
2 Chitsanzochi chikusonyeza bwino mkhalidwe umene mtundu wa anthu wakhalamo. Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, analengedwa angwiro. (Deuteronomo 32:4) Iwo anali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha ndi kukwaniritsa cholinga cha Mulungu chakuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Komabe, Adamu ndi Hava anapandukira Mlengi wawo. (Genesis 3:1-6) Kusamvera kwawo kunadzetsa uchimo osati pa Adamu ndi Hava okha komanso pa mbadwa zawo zimene zinali zisanabadwebe. Munthu wokhulupirika Yobu ananenera pambuyo pake kuti: “Adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.”—Yobu 14:4.
3. Kodi imfa inafalikira motani kwa anthu onse?
3 Choncho uchimo uli ngati nthenda imene yayambukira aliyense wa ife, popeza Baibulo limanena kuti ‘onse anachimwa.’ Zotsatirapo za mkhalidwewu n’zoikitsa moyo pachiswe. Ndithudi, “mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 3:23; 6:23) Palibe aliyense wa ife amene angaizembe. Anthu onse amachimwa, choncho, anthu onse amafa. Monga mbadwa za Adamu, tinabadwira m’tsoka limeneli. (Salmo 51:5) Paulo analemba kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tilibe chiyembekezo chilichonse cha chipulumutso.
Kuchotsa Uchimo ndi Imfa
4. Kodi n’chifukwa chiyani anthu paokha sangathetse matenda ndi imfa?
4 Kodi n’chiyani chingafunikire kuti uchimo ndi chotsatirapo chake imfa, zichotsedwe? Ndithudi, ndi chinthu china chimene palibe munthu aliyense angachipereke. Wamasalmo anadandaula kuti: “Malipo a moyo wa munthu ndi aakulu kwambiri. Zimene angapereke sizingakwanire kuti asaloŵe m’manda, kuti akhale kosatha.” (Salmo 49:8, 9, Today’s English Version) N’zoona kuti tingathe kutalikitsa moyo wathu ndi zaka zingapo mwa kudya zakudya zomanga thupi ndi kugwiritsa ntchito mankhwala, koma palibe aliyense wa ife amene angachotsepo mkhalidwe wauchimo wacholoŵa. Palibe aliyense wa ife amene angaimitse mphamvu yowononga thupi ya ukalamba ndi kubwezanso matupi athu kukhala angwiro monga momwe Mulungu anafunira pachiyambipo. Ndithudi Paulo sanakokomeze pamene analemba kuti chifukwa cha uchimo wa Adamu, anthu ‘anagonjetsedwa kuutsiru’—kapena monga momwe The Jerusalem Bible imanenera kuti, “analepheretsedwa kukwanitsa cholinga cha kukhalapo kwawo.” (Aroma 8:20) Koma mwamwayi, Mlengi sanatisiye. Iye wapanga makonzedwe ochotsapo uchimo ndi imfa kunthaŵi zonse. Motani?
5. Kodi Chilamulo chimene Israyeli anapatsidwa chinasonyeza motani kuti Yehova ndi wosamala kwambiri pa zachilungamo?
5 Yehova ndi “wakukonda chilungamo ndi chiweruzo.” (Salmo 33:5) Chilamulo chimene anapatsa Israyeli chimasonyeza kuti ndi wosamala kwambiri ndiponso sakondera pochita chilungamo. Mwachitsanzo, m’malamulo ameneŵa, timaŵerenga kuti ‘moyo uziperekedwa polipa moyo.’ M’mawu ena, ngati Mwisrayeli anapha munthu wina, moyo wa wakuphayo unayenera kuperekedwa polipa umene anachotsawo. (Eksodo 21:23; Numeri 35:21) Zikatero, chilungamo cha Mulungu chinali kukwaniritsidwa bwino.—Yerekezerani ndi Eksodo 21:30.
6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Adamu angatchedwe kuti wakupha? (b) Kodi Adamu anataya moyo wotani, ndipo ndi nsembe yotani imene inafunikira kukwaniritsa chilungamo?
6 Adamu atachimwa, anakhala wakupha. Chifukwa? Chifukwa chakuti anali kudzapatsira mkhalidwe wake wauchimowo—ngakhalenso imfa—kwa mbadwa zake zonse. N’kusamvera kwa Adamu kumene kukuchititsa kuti panopa matupi athu azimka namawonongeka, kuyandikira kumanda pang’onopang’ono. (Salmo 90:10) Uchimo wa Adamu umatanthauzanso chinachake chachikulu kwambiri. Kumbukirani, moyo umene Adamu ndi mbadwa zake anataya sunali moyo wamba wa zaka 70 kapena 80. Iye anataya moyo wangwiro—inde, moyo wosatha. Choncho ngati ‘moyo uyenera kulipa moyo,’ kodi ndi moyo wotani umene unayenera kuperekedwa kuti chilungamo chiyendetsedwe bwino panopa? Ndithudi, unayenera kukhala moyo wa munthu wangwiro—moyo umene, mofanana ndi wa Adamu, ukanatulutsa ana angwiro. Utaperekedwa monga nsembe, moyo wa munthu wangwiroyo sunali kudzangokwaniritsa chilungamo komanso unali kudzapangitsa kuti uchimo ndi chotsatirapo chake, imfa, zithe kufafanizidwa kotheratu.
Kulipira Mtengo wa Uchimo
7. Fotokozani tanthauzo la mawu akuti “dipo.”
7 M’Baibulo, mtengo wofunika kuti atiwombole ku uchimo umatchedwa kuti “dipo.” (Salmo 49:7) M’Chicheŵa mawuwo angatanthauze malipiro amene oweruza amafuna kuti amasule munthu wolakwa. Inde, dipo limene Yehova wapereka sililoŵetsapo oweruza ena. Koma lingaliro la kupereka malipiro ndi lomwelo. Ndipotu verebu lachihebri lotembenuzidwa kuti “dipo” kwenikweni limatanthauza “kuphimba.” Kuti uchimo ulipidwe, dipo liyenera kulingana ndendende ndi chinthu chimene likulipacho—moyo wangwiro wa Adamu.
8. (a) Fotokozani lamulo la kuwombola. (b) Kodi lamulo la kuwombola limatikhudza motani monga ochimwa?
8 Zimenezi n’zogwirizana ndi lamulo lopezeka m’Chilamulo cha Mose—lamulo la kuwombola. Ngati Mwisrayeli anakhala waumphaŵi nadzigulitsa yekha kukhala kapolo kwa munthu wosakhala Mwisrayeli, wachibale wake ankatha kumuwombola (kapena kuti, kumuperekera dipo) mwa kulipira mtengo wolingana ndi mtengo wa kapoloyo. (Levitiko 25:47-49) Baibulo limanena kuti monga anthu opanda ungwiro ndife “akapolo a uchimo.” (Aroma 6:6; 7:14, 25) Kodi chingafunikire n’chiyani potiwombola? Monga momwe taonera, kutayika kwa moyo waumunthu wangwiro kungafunikire malipo a moyo wa munthu wangwiro—basi.
9. Kodi Yehova wapanga motani makonzedwe ophimba uchimo?
9 Inde, anthufe timabadwa tili opanda ungwiro. Palibe aliyense wa ife amene ali ngati Adamu; palibe aliyense wa ife amene angalipe dipo limene chilungamo chikufuna. Monga momwe tatchulira poyamba, zili monga kuti tikudwala nthenda yakupha ndiponso sitingathe kulipira mtengo wa opaleshoni imene ingachotse nthendayo. Zitatere, kodi sitingayamikire wina ataloŵererapo ndi kulipira mtengowo? Ndizo zimene Yehova wachita! Iye wapanga makonzedwe otiwombola ku uchimo, kunthaŵi zonse. Inde, iye akufuna kutipatsa chinthu chimene sitingachipeze patokha. Motani? “Mphatso yaulere ya Mulungu,” analemba motero Paulo, “ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Yohane anafotokoza Yesu kukhala “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29) Tiyeni tione mmene Yehova anagwiritsira ntchito Mwana wake wokondedwa kulipira mtengo wa dipo.
“Dipo Lolingana”
10. Kodi maulosi onena za “mbewu” anadzasonya motani kwa Yosefe ndi Mariya?
10 Chipanduko chitangochitika mu Edene, Yehova analengeza za cholinga chake cha kupereka “mbewu,” kapena kuti mbadwa, imene idzawombola anthu ku uchimo. (Genesis 3:15) Mwa mavumbulutso angapo ochokera kwa iye, Yehova anasonyeza mzere wa banja limene lidzatulutsa mbewu imeneyi. M’kupita kwa nthaŵi mavumbulutso ameneŵa anasonya kwa Yosefe ndi Mariya, mwamuna ndi mkazi amene anali pafupi kukwatirana okhala ku Palestina. M’maloto, Yosefe anauzidwa kuti Mariya ali ndi pathupi mwa mzimu woyera. Mngeloyo anati: “Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”—Mateyu 1:20, 21.
11. (a) Kodi Yehova anachitanji kuti Mwana wake adzabadwe monga munthu wangwiro? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anatha kupereka “dipo lolingana”?
11 Pamenepa sipanali pathupi wamba, popeza kuti Yesu analipo kale kumwamba asanakhale munthu. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15) Moyo wake unasamutsidwira m’mimba mwa Mariya mwa mphamvu yozizwitsa ya Yehova, zikumachititsa kuti Mwana wokondedwa wa Mulungu ameneyu abadwe monga munthu. (Yohane 1:1-3, 14; Afilipi 2:6, 7) Yehova anayendetsa zinthu kuti Yesu asaipitsidwe ndi tchimo la Adamu. Choncho, Yesu anabadwa ali wangwiro. Chotero, iye anali ndi chimene Adamu anataya—moyo wangwiro waumunthu. Pomalizira pake, panali munthu wokhoza kulipira mtengo wa uchimo! Ndipo ndizo zimene Yesu anachita pa Nisani 14, 33 C.E. Patsiku lokumbukika limenelo, Yesu analola kuphedwa ndi adani ake, mwakutero akumapereka “dipo lolingana.”—1 Timoteo 2:6, NW.
Mtengo wa Moyo Wangwiro Waumunthu
12. (a) Fotokozani kusiyana kofunika kwambiri pakati pa imfa ya Yesu ndi imfa ya Adamu. (b) Kodi Yesu wakhala motani “Atate Wosatha” kwa anthu omvera?
12 Pali kusiyana pakati pa imfa ya Yesu ndi imfa ya Adamu—kusiyana kumene kukusonyeza mtengo wa dipo. Adamu anayenerera kufa, popeza kuti anasankha kusamvera Mlengi wake. (Genesis 2:16, 17) Koma Yesu sanayenerere kufa mpang’ono pomwe, popeza kuti “sanachita tchimo.” (1 Petro 2:22) Choncho pamene Yesu anafa, iye anali ndi chinachake cha mtengo waukulu kwambiri chimene Adamu wochimwayo analibe pa imfa yake—ufulu wokhala ndi moyo wangwiro waumunthu. Choncho, imfa ya Yesu inali nsembe. Atapita kumwamba monga munthu wauzimu, iye anapereka mtengo wa nsembe yake kwa Yehova. (Ahebri 9:24) Mwa kuchita zimenezo, Yesu anawombola anthu ochimwa nakhala Atate wawo watsopano, woloŵa m’malo mwa Adamu. (1 Akorinto 15:45) Ndiyetu chifukwa chake Yesu amatchedwa kuti “Atate Wosatha.” (Yesaya 9:6) Tangolingalirani tanthauzo la zimenezo! Adamu, atate wochimwa, anapatsira mbadwa zake zonse imfa. Yesu, Atate wangwiro, amagwiritsa ntchito mtengo wa nsembe yake kupereka moyo wosatha kwa anthu omvera.
13. (a) Perekani chitsanzo cha mmene Yesu anaperekera malipo a ngongole ya Adamu. (b) Kodi n’chifukwa chiyani nsembe ya Yesu siwombola makolo athu oyamba ku tchimo lawo?
13 Komano kodi zinatheka bwanji kuti imfa ya munthu mmodzi n’kulipa machimo a anthu ambiri? (Mateyu 20:28) M’nkhani ina zaka zingapo zapitazo, tinayerekeza dipo motere: “Yerekezerani kuti pali fakitale yaikulu yokhala ndi antchito ambirimbiri. Manijala wosaona mtima wa fakitaleyo waba ndalama za malondawo; fakitaleyo n’kutsekedwa. Anthu ambirimbiri tsopano ali paulova ndipo satha kulipira ngongole zawo. Anzawo a muukwati, ana, ngakhalenso onse amene anawakongoza ndalama akuvutika chifukwa cha kusaona mtima kwa munthu mmodzi uja! Ndiyeno pakubwera wowawonjola wachuma amene akubweza ngongole zonse za kampani ndi kutsegulanso fakitaleyo. Kulipidwa kwa ngongole imodziyo, tsopano, kwadzetsa mpumulo waukulu kwa antchito ambirimbiriwo, mabanja awo, ndi owakongoza ndalama. Koma kodi manijala woyamba uja nayenso akupindula ndi chuma chatsopanocho? Ayi, iye ali m’ndende, choncho ntchito yake inatheratu! Mofananamo, kulipidwa kwa ngongole imodzi ya Adamu kwadzetsa mapindu kwa mbadwa zake miyandamiyanda—koma osati kwa Adamu.”
14, 15. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Adamu ndi Hava anachimwa dala, ndipo mkhalidwe wathu n’ngwosiyana motani ndi wawo?
14 Chimenechi n’chilungamo. Kumbukirani kuti Adamu ndi Hava anachimwa dala. Iwo anasankha kusamvera Mulungu. Koma ife timabadwira mu uchimo. Palibe zimene tingachite. Kaya tiyesetse zotani, sitingapeŵeretu kuchimwa. (1 Yohane 1:8) Nthaŵi zina timamva ngati Paulo, amene analemba kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga. Munthu wosauka ine.”—Aroma 7:21-24.
15 Komabe, chifukwa cha dipo, tili ndi chiyembekezo! Yesu ndiye mbewu mwa imene, monga Mulungu analonjeza, “mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:18; Aroma 8:20) Nsembe ya Yesu imapatsa awo amene amam’khulupirira mwayi wa zinthu zosangalatsa kwambiri. Tiyeni tikambirane zina mwa zimenezi.
Kupindula ndi Dipo la Kristu
16. Ngakhale kuti ndife ochimwa, kodi ndi mapindu otani amene tili nawo tsopano chifukwa cha dipo la Yesu?
16 Wolemba Baibulo Yakobo anavomereza kuti “timakhumudwa tonse pazinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Koma chifukwa cha dipo la Kristu, zolakwa zathu zimakhululukidwa. Yohane analemba kuti: “Akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu.” (1 Yohane 2:1, 2) Komatu sitiyenera kupeputsa uchimo. (Yuda 4; yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:27.) Koma ngati tachimwa, tingatsanulire mtima wathu kwa Yehova, tili ndi chidaliro chakuti iye ali “wokhululukira.” (Salmo 86:5; 130:3, 4; Yesaya 1:18; 55:7; Machitidwe 3:19) Choncho dipo limatipangitsa kutumikira Mulungu ndi chikumbumtima chabwino ndipo limatipangitsa kum’fikira m’pemphero kudzera m’dzina la Yesu Kristu.—Yohane 14:13, 14; Ahebri 9:14.
17. Chifukwa cha dipo, kodi m’tsogolo mudzakhala madalitso otani?
17 Dipo la Kristu likutsegula njira yokwaniritsira cholinga cha Mulungu—choti anthu omvera akhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:29) Paulo analemba kuti: “Mosasamala kanthu za unyinji wa malonjezo a Mulungu, iwo akhala Inde mwa iye [Yesu].” (2 Akorinto 1:20, NW) N’zoona kuti imfa “inachita ufumu.” (Aroma 5:17) Dipo limapatsa Mulungu maziko ochotsera “mdani wotsiriza” ameneyu. (1 Akorinto 15:26; Chivumbulutso 21:4) Dipo la Yesu lingapindulitsenso awo amene anamwalira. “Ikudza nthaŵi,” anatero Yesu, “imene onse ali m’manda adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; 1 Akorinto 15:20-22.
18. Kodi uchimo wadzetsa mavuto otani pa anthu, ndipo kodi zimenezi zidzathetsedwa motani m’dziko latsopano la Mulungu?
18 Talingalirani kusangalatsa kwa kukhala ndi moyo monga momwe unayenera kukhalira—wopanda nkhaŵa zimene zikutithodwetsa lerolino! Uchimo sunatisokonezere chabe unansi wathu ndi Mulungu komanso wasokoneza maganizo athu, mtima wathu, ndi thupi lathu. Komabe, Baibulo limalonjeza kuti m’dziko latsopano la Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Inde, matenda akuthupi ndi zinthu zopsinja maganizo sizidzavutitsanso anthu. Chifukwa chiyani? Yesaya akuyankha kuti: “Anthu okhala mmenemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.”—Yesaya 33:24.
Dipo—Chisonyezero cha Chikondi
19. Kodi aliyense wa ife ayenera kuchitaponji pa dipo la Kristu?
19 Chikondi chinasonkhezera Yehova kutitumizira Mwana wake wokondedwa. (Aroma 5:8; 1 Yohane 4:9) Komanso chikondi chinasonkhezera Yesu kuti “alaŵe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Ahebri 2:9; Yohane 15:13) Ndiye chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza . . . Adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) Ngati tikuyamikira zimene Yesu anatichitira, tidzachitapo kanthu. Ndipotu dipo likupangitsa kuti tipulumutsidwe ku imfa! Ndithudi sitingafune kuti mwa zochita zathu tisonyeze kuti nsembe ya Yesu timaiona ngati chinthu wamba.—Ahebri 10:29.
20. Kodi ndi njira zina ziti zimene timasungira “mawu” a Yesu?
20 Kodi tingasonyeze motani kuti dipo timaliyamikira kuchokera pansi pa mtima? Atatsala pang’ono kumangidwa, Yesu anati: “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mawu anga.” (Yohane 14:23) “Mawu” a Yesu amaphatikizapo lamulo lake lonena kuti tizitengamo mbali mwachangu pokwaniritsa ntchitoyi: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo.” (Mateyu 28:19) Kumvera Yesu kumafunanso kuti tizisonyeza chikondi kwa abale athu auzimu.—Yohane 13:34, 35.
21. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pa phwando la Chikumbutso pa April 1?
21 Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zimene tingasonyezere kuti dipo timaliyamikira ndiyo mwa kupezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, chimene chaka chino chidzakhalako pa April 1.a Chimenechonso chili mbali ya “mawu” a Yesu, popeza kuti poyambitsa phwando limeneli, Yesu analamula otsatira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Mwa kupezeka pa chochitika chofunika koposa chimenechi ndiponso mwa kutsatira mosamalitsa zonse zimene Kristu anatilamula, tidzasonyeza kuti timakhulupirira zedi kuti dipo la Yesu ndilo njira ya Mulungu ya chipulumutso. Ndithudi, “palibe chipulumutso mwa wina yense.”—Machitidwe 4:12.
[Mawu a M’munsi]
a Chaka chino, April 1 ndilo tsiku lolingana ndi Nisani 14, 33 C.E., tsiku limene Yesu anafa. Funsani Mboni za Yehova za kwanuko ponena za nthaŵi ndi malo a phwando la Chikumbutso.
Kodi Mungakumbukire?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani anthu sangapereke dipo la uchimo wawo?
◻ Kodi Yesu ndi “dipo lolingana” m’njira yotani?
◻ Kodi Yesu anatipindulitsa motani ndi ufulu wake wokhala ndi moyo wangwiro waumunthu?
◻ Kodi ndi madalitso otani amene amadza kwa mtundu wa anthu chifukwa cha dipo la Kristu?
[Chithunzi patsamba 15]
Munthu wangwiro yekha—wolingana ndi Adamu—ndi amene anakhutiritsa chilungamo
[Chithunzi patsamba 16]
Popeza kuti Yesu anali ndi ufulu wokhala ndi moyo wangwiro waumunthu, imfa yake inali nsembe