Ndandanda ya Mlungu wa July 15
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 15
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 26 ndime 1-8 ndi bokosi patsamba 204 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 18–21 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 20:17-38 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu Adzaona Khristu Akubwera M’mitambo Kudzatenga Akhristu Okhulupirika Kupita Nawo Kumwamba?—rs mutu womalizira pa tsa. 213 mpaka tsa. 214 ndime 3. (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timaika Maganizo Athu pa Zinthu za Mzimu?—Aroma 8:6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Mufikeni Pamtima Wophunzira Wanu. (Luka 24:32) Nkhani yokambirana yochokera pa mafunso awa: (1) Mukamachititsa phunziro la Baibulo, n’chifukwa chiyani m’pofunika kutsindika (a) Chikondi ndi nzeru za Yehova? (b) kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo? (c) Kufunika koti nthawi zonse tizifufuza malangizo a Yehova tisanasankhe zochita? (2) Kodi kufunsa wophunzira wanu mafunso otsatirawa kungakuthandizeni bwanji kuti mudziwe ngati mukumufikadi pa mtima? (a) Kodi inuyo mukuona kuti zimenezi n’zoona? (b) Kodi mukuona kuti zimenezi n’zogwirizana ndi chikondi cha Mulungu? (c) Kodi mukuganiza kuti kutsatira malangizo amenewa kungakuthandizeni bwanji?
Mph. 20: “Abale Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kuti Muyenerere Udindo mu Mpingo?” Mafunso ndi mayankho. Funsani mwachidule mkulu kapena mtumiki wothandiza amene anayamba ali wachinyamata kuyesetsa kuti ayenerere udindo mu mpingo. Kodi ndi ntchito ziti zimene anapatsidwa asanakhale mtumiki wothandiza ndipo anaphunzitsidwa bwanji kugwira ntchitozo? Kodi anthu ena mu mpingo anamuthandiza bwanji kuti apite patsogolo mwauzimu? Ndi madalitso ati amene wapeza chifukwa choyesetsa kuti ayenerere udindo mu mpingo?
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero