Ndandanda ya Mlungu wa August 5
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 5
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 27 ndime 1-9 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Aroma 1-4 (Mph. 10)
Na. 1: Aroma 3:21–31 mpaka 4:1-8 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amadziona Ngati “Alendo Ndiponso Anthu Osakhalitsa M’dzikoli”?—1 Pet. 2:11; 1 Yoh. 2:15-17 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Akhristu Oona Adzatetezedwa Bwanji pa Chisautso Chachikulu?—rs tsa. 216 ndime 2-6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu August. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi lomwe angafunse ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Luka 5:27-32. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki wakumunda.
Nyimbo Na. 119 ndi Pemphero