Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Mayani Hill itamangidwa m’dera la C-19 ku Dedza, mfumu ya deralo inayamikira gulu lathu chifukwa chomanga nyumba yokongola kwambiri m’dera lake. Mfumuyi inachita chidwi ndi kukongola komanso kulimba kwa nyumbayi ndipo inanena kuti anthu amene ankagwira ntchito yomanga nyumbayi anali ogwirizana. Khalidwe limeneli linathandiza anthu a m’derali kuzindikira kuti anthuwa ndi Akhristu oona. Pofika pano Nyumba za Ufumu zoposa 1,070 zamangidwa m’Malawi muno. Koma kodi udindo wathu ndi wotani? Tiyenera kupitiriza kusamalira malo abwino olambirirapowa amene Yehova watipatsa kudzera m’gulu lake.—1 Mbiri 29:1-5, 8, 9.