Ndandanda ya Mlungu wa September 9
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 9
Nyimbo Na. 13 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 28 ndime 16-22 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Akorinto 10-16 (Mph. 10)
Na. 1: 1 Akorinto 14:7-25 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Munthu Wochimwa ‘Akhazikitse Pansi Mtima wa Yehova’?—2 Mbiri 33:12, 13; Yes. 55:6, 7 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Sitinganene Kuti Lemba la Yohane 9:1, 2 Limasonyeza Kuti Munthu Amabadwanso Kwinakwake?—rs tsa. 176 ndime 2-tsa. 177 ndime 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?—Gawo 1. Nkhani yochokera m’kapepala kakuti Moyo Wanu ndime 1-9. Ayamikireni ndi mtima wonse achinyamata obatizidwa amene akuyesetsa kuika zinthu za Ufumu patsogolo.
Mph. 10: Zokumana nazo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pogwiritsa ntchito kabuku ka Uthenga Wabwino poyambitsa phunziro la Baibulo. Chitaninso chitsanzo chosonyeza mmene mungapangire ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira magazini athu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013 patsamba 7.
Mph. 10: “Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Amosi.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero