Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Amosi
1. N’chifukwa chiyani chitsanzo cha mneneri Amosi chili cholimbikitsa kwambiri?
1 Kodi munayamba mwamvapo ngati kuti ndinu wosayenera kulalikira mwina chifukwa choti simunaphunzire kwambiri kapena munakulira m’banja losauka? Ngati ndi choncho, chitsanzo cha mneneri Amosi chikhoza kukulimbikitsani. Iye anali woweta nkhosa ndipo pa nyengo ina chaka chilichonse ankagwiranso ntchito zina zakumunda. Komabe Yehova anamuthandiza kukhala wolimba mtima kuti akalalikire uthenga wofunika kwambiri kwa Ayuda. (Amosi 1:1; 7:14, 15) Masiku anonso, Yehova amagwiritsa ntchito anthu wamba kuti agwire ntchito yolalikira. (1 Akor. 1:27-29) Kodi tingaphunzirenso zinthu zina ziti zokhudza utumiki wathu kuchokera kwa mneneri Amosi?
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe olimba tikamatsutsidwa mu utumiki?
2 Khalanibe Olimba Mukamatsutsidwa: Amaziya yemwe anali wansembe wopembedza mwana wa ng’ombe mu ufumu wakumpoto wa mafuko 10 a Isiraeli, atamva za uthenga womwe Amosi ankanenera, anayankha ndi mawu omwe angafanane ndi akuti, ‘Choka pano, pita kwanu usativutitse. Ife tili ndi chipembedzo chathu.’ (Amosi 7:12, 13) Ndiyeno Amaziya ananena kwa Mfumu Yeroboamu zinthu zabodza zokhudza uthenga umene Amosi ankalalikira n’cholinga choti mfumuyo imuletse kulalikira. (Amosi 7:7-11) Koma Amosi sanachite mantha. Masiku anonso, atsogoleri ena azipembedzo amapempha mabungwe andale kuti azithandiza nawo kuzunza atumiki a Yehova. Komabe, Yehova amatitsimikizira kuti palibe chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chitivulaze chimene chidzapambane.—Yes. 54:17.
3. Kodi uthenga umene timalengeza masiku ano umanena za zinthu ziwiri ziti?
3 Muzilalikira za Chiweruzo cha Mulungu Komanso za Madalitso a M’tsogolo: Ngakhale kuti mneneri Amosi ankalengeza uthenga wa chiweruzo wokhudza ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli, kumapeto kwa buku limene analembali, iye anatchula za lonjezo la Yehova loti adzadzutsanso nyumba ya Davide imene inagwa komanso kuti adzaidalitsa kwambiri. (Amosi 9:13-15) Ifenso tikamalalikira, timanena za “tsiku la chiweruzo” la Mulungu lomwe likubwera. Koma imeneyi ndi mbali imodzi chabe ya “uthenga wabwino wa ufumu” umene tiyenera kulengeza. (2 Pet. 3:7; Mat. 24:14) Yehova akadzawononga anthu oipa pa nkhondo ya Aramagedo, zidzatsegula njira yoti dziko lino likhale paradaiso.—Sal. 37:34.
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti tidzakwanitsa kuchita chifuniro cha Yehova?
4 Tikamalalikira za Ufumu m’dzikoli lomwe muli anthu ambiri otsutsa zimakhala zovuta kwambiri kukhala odzipereka kwa Yehova komanso kuchita chifuniro chake. (Yoh. 15:19) Ngakhale zili choncho, sitikayikira kuti Yehova adzatipatsa zonse zofunikira kuti tikwanitse kuchita chifuniro chake ngati mmene anachitira ndi mneneri Amosi.—2 Akor. 3:5.