Ndandanda ya Mlungu wa September 16
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 16
Nyimbo Na. 115 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 1 ndime 1-7 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Akorinto 1-7 (Mph. 10)
Na. 1: 2 Akorinto 1:15-24 mpaka 2:1-11 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Pali Kusiyana Kotani Pakati pa Chikhulupiriro Chakuti Munthu Akafa Amakabadwanso Kwinakwake, Ndi Chiyembekezo cha M’Baibulo?—rs tsa. 177 ndime 4-tsa. 178 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Munthu Angatani Kuti Apeze Chitetezo M’dzina la Yehova?—Zef. 3:12 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?—Gawo 2. Nkhani yochokera m’kapepala kakuti Moyo Wanu, kuyambira ndime 10 mpaka kumapeto kwa nkhaniyo. Funsani mwachidule munthu amene anachitapo utumiki wa nthawi zonse ali wachinyamata. Kodi n’chiyani chinamuchititsa kuti asankhe kuchita utumiki umenewo? Kodi anapeza madalitso otani?
Mph. 10: Mukamalalikira Nokha. Nkhani yokambirana. (1) N’chiyani chingatithandize kukhalabe osangalala tikamalalikira tokha? (2) Kodi tiyenera kusamala ndi zinthu ngati ziti tikamapanga maulendo obwereza tili tokha? (3) Ngati palibe amene amalowa mu utumiki masiku amene ife timalowa, kodi tingalimbikitse bwanji anthu ena mu mpingo kuti azilowa nafe mu utumiki? (4) Kodi nthawi zina kulalikira tokha ngati palibe zovuta zilizonse kuli ndi ubwino wotani?
Mph. 10: “Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ngati ladziwika.
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero