Kudziveka Thupi Lanyama
Tanthauzo: Chikhulupiriro chakuti munthu amabadwa kachiŵiri m’kukhalapo kumodzi kapena kuposa kotsatizanatsatizana, kumene kungakhale mwa munthu kapena nyama. Kaŵirikaŵiri ndiwo “moyo” wosawonekawo umene umakhulupiriridwa kubadwanso m’thupi lina. Sichiri chiphunzitso cha Baibulo.
Kodi lingaliro lachilendo la kukhala ozoloŵerana ndi mabwenzi ndi malo atsopano kotheratu limatsimikizira kudzviveka thupi lanyama kukhala kotsimikizirika?
Kodi munayamba mwafanizirapo mwamuna wina kapena mkazi wamoyo ndi munthu wina amenenso ali moyo tsopano? Ochuluka akhala ndi chokumana nacho chotero. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu ena ali ndi zizoloŵezi zofanana kapena angawonekere kukhala pafupifupi ofanana. Chotero lingaliro lakuti mumadziŵa munthuyo ngakhale kuli kwakuti simunakumanepo naye kale silimatsimikiziradi kuti munali wozoloŵerana naye m’moyo wapapitapo, kodi sichoncho?
Kodi nchifukwa ninji nyumba kapena tauni ingawonekere kukhala yozoloŵereka kwa inu ngati simunakhale kumeneko konse? Kodi chiri chifukwa chakuti munakhala kumeneko m’nthaŵi ya moyo wanu woyamba? Nyumba zambiri zimamangidwa motsatira mapangidwe ofanana. Mipando yogwiritsiridwa ntchito m’mizinda yotalikirana ingakhale yopangidwa kuchokera ku zitsanzo zofanana. Ndipo kodi sizowona kuti malo okongola m’zigawo zotalikirana kwambiri amawonekera kukhala ofanana kwambiri? Motero, popanda kufunikira kuvekedwa thupi lanyama, malingaliro anu a kufanana kwa malo ali ndi chifukwa chabwino kwambiri.
Kodi zikumbukiro za moyo panthaŵi ina pamalo ena, monga momwe zimatulutsidwira ndi munthu atatsirikidwa, zimatsimikizira kudziveka thupi?
Pamene munthu atsirikidwa unyinji wa chidziŵitso chosungidwa muubongo wake ungakhoze kutulutsidwa. Otsirikawo amagwira kuganiza kwa munthuyo. Koma kodi zinthu zokumbukiridwa zimenezo zinafikamo motani? Mwinamwake munaŵerenga bukhu, munawona chithunzi chakanema, kapena kuphunzira za anthu ena patelevizheni. Ngati inu mudziika mmalo a anthu ponena za amene munali kuphunzira, kungakhale kutachititsa kukhomerezeka kwakukulu, pafupifupi ngati kuti chochitikacho chinali cha inu mwini. Zimene kwenikweni inu munachita zingakhale zakalekale kotero kuti mwaziiŵala, koma mutatsirikidwa chochitikacho chingakumbukike monga ngati kuti munali kukumbukira “moyo.” Komabe, ngati zimenezo zinali zowona, kodi aliyense sakanakhala ndi zikumbukiro zotero? Koma siyense amene amatero. Nkokondweretsa kuwona kuti chiŵerengero chowonjezereka cha makhothi apamwamba a zigawo m’United States sichimavomereza umboni woperekedwa munthu atatsirikidwa. Mu 1980 Khothi Lapamwamba la m’Minnesota linalengeza kuti “umboni wabwino koposa wa katswiri umasonyeza kuti palibe katswiri amene angatsimikizire kuti kaya chikumbukiro chochititsidwa ndi kutsirikidwa, kapena mbali iriyonse ya chikumbukirocho, uli wowona, wonama, kapena nthano—kungodzadza malingaliro ndi nthano. Zotulukapo zotero siziri zodalirika moyenerera kukhala zolondola.” (State v. Mack, 292 N.W.2d 764) Chisonkhezero cha malingaliro opangidwa ndi otsirika kwa munthu wotsirikidwayo ndicho chochititsa kusadalirika kumeneku.
Kodi Baibulo liri ndi umboni wa kukhulupirira kudziveka thupi lanyama?
Kodi Mateyu 17:12, 13 akupereka maziko a kukhulupirira kudziveka thupi lanyama?
Mat. 17:12, 13: “[Yesu anati,] Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziŵa iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo. Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nawo za Yohane Mbatizi.”
Kodi izi zinatanthauza kuti Yohane Mbatizi anali Eliya wovalanso thupi lanyama? Pamene ansembe Achiyuda anafunsa Yohane kuti, “ndiwe Eliya kodi?” iye anati, “sindine iye.” (Yoh. 1:21) Pamenepa, kodi chiyani, chimene Yesu anatanthauza? Monga momwe mngelo wa Yehova adaneneratu, Yohane anapita patsogolo pa Mesiya wa Yehova “ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana awo, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.” (Luka 1:17) Chotero Yohane Mbatizi anali kukwaniritsa ulosi mwa kuchita ntchito yofanana ndi ija ya mneneri Eliya.—Mal. 4:5, 6.
Kodi kudziveka thupi lanyama kwasonyezedwa ndi cholembedwa pa Yohane 9:1, 2?
Yoh. 9:1, 2 amati: “Ndipo popita [Yesu] anawona munthu ali wosawona chibadwire. Ndipo akuphunzira ake anamfunsa iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosawona?”
Kodi kungakhale kothekera kuti ophunzira amenewa anali atasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro cha Afarisi Achiyuda, amene ananena kuti “miyoyo ya anthu abwino imangosamutsidwira kokha m’matupi ena”? (Wars of the Jews, Josephus, Book II, mutu VIII, ndime 14) Sikukuwonekera choncho, chifukwa chakuti funso lawo silikupereka tanthauzo lakuti iwo analingalira kuti iyeyu anali ‘munthu wabwino.’ Kuli kwachiwonekere kwambiri kuti monga ophunzira a Yesu iwo anakhulupirira Malemba ndipo anadziŵa kuti miyoyo imafa. Komabe, popeza ngakhale khanda m’mimba liri ndi moyo ndipo linakhaliridwa pakati muuchimo, iwo angakhale atadabwa kuti kaya mwana wosabadwa wotero angakhale atachimwa, kukumachititsa kukhala kwake wakhungu. Mulimonse, yankho la Yesu silinachirikize kaya kudziveka thupi lanyama kapena lingaliro lakuti mwana amene sanabadwe m’mimba mwa amake amachimwa asanabadwe. Yesu mwiniyo anayankha kuti: “Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake.” (Yoh. 9:3) Yesu anadziŵa kuti, chifukwa chakuti ndife mbadwa za Adamu, pali choloŵa cha zophophonya ndi kupanda ungwiro za umunthu. Akumagwiritsira ntchito mkhalidwewo kukuza Mulungu, Yesu anachiritsa munthu wakhunguyo.
Kodi chiphunzitso cha Baibulo chonena za moyo ndi imfa chimapereka mpata wa kudziveka thupi lanyama?
Genesis 2:7 amalongosola kuti: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” Tawonani kuti munthu iyemwiniyo anali moyo; moyowo suunali pawokha wolekana ndi wosiyana ndi thupi. “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezek. 18:4, 20) Ndipo munthu wakufa amanenedwa kukhala “moyo wakufa.” (Num. 6:6, NW) Pa imfa, “mpweya uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Sal. 146:4) Chotero pamene munthu amwalira, munthu wathunthu wafa; palibe chirichonse chimene chimatsala cha moyo ndi chimene chikanapitirizidwira m’thupi lina. (Kaamba ka maumboni owonjezereka, wonani nkhani yaikulu yakuti “Moyo” ndi “Imfa.”)
Mlal. 3:19: “Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale choŵagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso.” (Monga momwe ziri m’chochitika cha anthu, palibe chimene chimapulumuka pa imfa ya zinyama. Palibe chimene chingakhale ndi kubadwanso m’thupi lina.)
Mlal. 9:10: “Chirichonse dzanja lako lichipeza kuchita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda uli kupitako.” (Akufa samapita m’thupi lina koma m’Sheoli, manda a anthu onse.)
Kodi nkusiyana kokulira kotani kumene kulipo pakati pa kudziveka thupi lanyama ndi chiyembekezo choperekedwa m’Baibulo?
Kudziveka thupi lanyama: Mogwirizana ndi chikhulupiriro ichi, pamene munthu afa, moyo, “munthu mwiniyo,” amapitirira kumka kumoyo wabwinopo ngati munthuyo anali ndi moyo wabwino ndi woyenerera, koma mwinamwake amakakhala nyama ngati mbiri yake inali yoipa kwambiri. Kukukhulupiriridwa kuti, kubadwanso kulikonse, kumabwezeretsa munthuyo m’dongosolo limodzimodzilo, mu limene iye adzayang’anizananso ndi kuvutika kowonjezereka ndipo potsirizira pake imfa. Zungulirezungulire wa kubadwanso kwakukulukulu amawonedwa kukhala wopanda mapeto. Kodi mtsogolo motero ndimo mmene mukukuyembekezerani? Ena amakhulupirira kuti njira yokha ya kuwonjokera ndiyo kuzima chikhumbo chonse cha zinthu zokondweretsa maganizo. Kodi iwo amathaŵira kuti? Kumoyo umene ena amafotokoza kuti wa kusadziŵa.
Baibulo: Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, moyo ndiye munthu wathunthu. Ngakhale ngati munthuyo angakhale atachita zinthu zoipa m’nthaŵi zapita, koma ngati iye alapa nasintha njira zake, Yehova Mulungu adzamkhululukira. (Sal. 103:12, 13) Pamene munthu amwalira, palibe chimene chimatsala. Imfa iri ngati tulo tatikulu, topanda maloto. Kudzakhala chiukiriro cha akufa. Chimenechi sindicho kuvalidwanso kwathupi lanyama koma kubwezeredwanso moyo kwa munthu mmodzimodziyo. (Mac. 24:15) Kwa anthu ambiri, chiukiriro chidzakhala moyo padziko lapansi. Chidzachitika Mulungu atadzetsa mapeto a dongosolo loipa liripoli lazinthu. Kudwala, matenda, ngakhale kufunikira kufa, zidzatha. (Dan. 2:44; Chiv. 21:3, 4) Kodi chiyembekezo chotero chimamvekera ngati kanthu kena kamene mukanafuna kuphunzirira zowonjezereka, kupenda zifukwa zodalirira?
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Ndimakhulupirira m’kudziveka thupi lanyama’
Mungayankhe kuti: ‘Mukhulupirira kuti potsirizira pake kudzachititsa m’moyo wabwino kwambiri, kodi sichoncho? . . . Tandiuzani, kodi mukanakonda kukhala ndi moyo m’dziko lofanana ndi limene lalongosoledwa pano pa Chivumbulutso 21:1-5?’
Kapena munganene kuti: ‘Ndikuyamikira kundiuza kwanu zimenezo. Tandilolani ndikufunseni, Kodi zimenezi ziri kanthu kena kamene mwakhulupirira nthaŵi zonse? . . . Kodi nchiyani chimene chinakupangitsani kusiya zikhulupiriro zanu zoyamba?’ (Ndiyeno mwinamwake gwiritsirani ntchito malingaliro pamutuwu pa tsamba 177.)
Kuthekera kwina: ‘Ndasangalala kukambitsirana ndi ena amene ali ndi chikhulupiriro chimenecho. Tandilolani ndikufunseni, Kodi nchifukwa ninji mumalingalira kuti kudziveka thupi lanyama kuli kofunika?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani: (1) ‘Kodi mukukumbukira tsatanetsatane yense wa moyo woyambirira umene mukulingalira kuti munali nawo? . . . Koma zimenezo zikakhala zofunika ngati munthuyo ati akalungamitse zolakwa zake zoyamba ndi kuwongolera, kodi sichoncho?’ (2) Ngati munthu anena kuti kuli kukoma mtima kuti tiiŵale, mungafunse kuti: ‘Komatu inu mumawona kuti kukumbukira chinthu choipa kungakhale phindu kwa munthu m’moyo watsiku ndi tsiku? Ndiyeno mwakuiŵala zaka 70 ziri zonse kapena zoposerapo zimene taziphunzira, kodi tikathandizidwa kuwongolera mkhalidwe wathu?’ (3) Ngati munthuyo anena kuti ali anthu abwino kwambiri okha amene amabadwanso monga anthu, inu mungafunse kuti: ‘Nangano, nchifukwa ninji, mikhalidwe yadziko yapitirizabe kuipiraipira? . . . Baibulo limasonyeza mmene kuwongokera kwenikweni kudzapangidwira m’tsiku lathu. (Dan. 2:44)’