Kodi Kubadwanso kwa Moyo Ndiko Mfungulo ya Zinsinsi za Moyo?
Kodi munayamba mwakhalako?
Kodi mudzakhalakonso mumtundu wina wa moyo mutafa?
Mafunso ameneŵa angakumbutse za chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo.
The New Encyclopædia Britannica imamasulira “kubadwanso kwa moyo” mwanjira yotsatirayi: “Chikhulupiriro cha kubadwa kwatsopano kwa moyo mwa kukhalako kamodzi kapena kambiri motsatizanatsatizana, kumene kungakhale kwaumunthu, nyama, kapena, nthaŵi zina, zomera.”
Kubadwanso kwa moyo nkofunika kwambiri m’zipembedzo Zakummaŵa, makamaka zija zimene zinayambira ku India, zonga Chibudha, Chihindu, Chijain, ndi Chisikh. Mwachitsanzo, pakati pa Ahindu ku India, moyo umalingaliridwa kukhala njira yosatha ya kufa ndi kubadwanso.
Komabe, posachedwapa, lingaliro la kubadwanso kwa moyo lachititsa chidwi ambiri okhala ku Chigawo Chadziko Chakumadzulo, kuphatikizapo achichepere ochulukirapo. Malinga ndi kunena kwa wolemba nkhani wina mu Sunday Star ya ku Canada, chifukwa chochititsa kukopeka kwakukulu kumeneku “ndicho zotsatirapo za chiyambukiro cha zikhulupiriro zachipembedzo Zakummaŵa pa chitaganya chathu Chakumadzulo, chimene chinayamba m’ma 1960.”
Chifukwa china chochititsa kukopeka ndi kubadwanso kwa moyo nchakuti akatswiri ena anena poyera ndi motsimikiza kuti anakhalako ndi moyo kamodzi kapena kambiri papitapo. Ndiponso, wailesi, TV, magazini, ndi njira zina zofalitsira nkhani zasonyeza kukopeka ndi kubadwanso kwa moyo, monga momwe achitira akatswiri ambiri onga madokotala ndi aphunzitsi.
Zonsezi zachititsa chidwi kwambiri. Chotero, malinga ndi kufufuza kwina, pafupifupi limodzi la magawo anayi a anthu m’Canada ndi United States lavomereza kuti mwanjira ina yake limakhulupirira kubadwanso kwa moyo.
Zonenedwa pa Zochitika za Moyo Wapapitapo
Woseŵera mafilimu Shirley MacLaine pofunsidwa ndi Phyllis Battelle mu Ladies’ Home Journal ananena kuti wapanga “maulendo” angapo kupita ku nthaŵi zakale. “Ndikukumbukira miyoyo yanga yambiri yapapitapo—panthaŵi ina ndinali mwamuna, nthaŵi ina ndinali mkazi,” iye anatero.
M’buku lakuti Coming Back, Dr. Raymond Moody anafotokoza kuyesa kumene anachita pa ophunzira ake ndi ena. Ananena kuti mwa kuwagoneka tulo iye anawatengera ku nthaŵi imene anali asanabadwe, ndipo iwo ananena kuti anakumbukira miyoyo yawo yapapitapo. Munthu wina ananena kuti anakhalako monga Mweskimo m’chitaganya cha Aeskimo. Wina anati anakhalako m’nthaŵi ya ‘stone age,’ zaka zikwi zambiri zapitazo.
Dr. Moody mwiniyo ananena kuti anakhala ndi miyoyo isanu ndi inayi papitapo. Imeneyi inali yosiyanasiyana kuyambira moyo wa m’mitengo monga “mtundu wa munthu wamakedzana wosatsungula” kufikira moyo wa m’masiku a ufumu wa Roma, pamene, iye anatero, anagwidwa ndi kujiwa ndi mkango m’bwalo lamaseŵera.
Kugwiritsira ntchito njira yogoneka tulo kutengera anthu ofuna kudziŵa ku nthaŵi yongoyerekezera yakale asanabadwe kwafotokozedwanso kukhala kopindulitsa kwa ena. Madokotala aigwiritsira ntchito kuchiritsira matenda amaganizo. Kukunenedwa kuti mantha osadziŵika athetsedwa mwa kupeza magwero a vutolo m’chochitika chinachake m’moyo wapapitapo. Kodi lingaliro limeneli n’loona motani?
Zoonedwa Pamene Munthu Atsala Pang’ono Kufa Zosimbidwa
Zoonedwa pamene munthu atsala pang’ona kufa zosimbidwa ndi anthu ena zatchukitsa chikhulupiriro cha kubadwanso kwa moyo. M’buku lakuti Life After Life, Dr. Moody akusimba zopeza zake ponena za zoonedwa pamene munthu atsala pang’ono kufa zosimbidwa ndi anthu pafupifupi 50.
Pamene kuli kwakuti zoonedwa zawo zakhala zosiyana, Moody akuganiza kuti zili ndi njira yofanana. Anthu ameneŵa anali kuona monga ngati kuti akuyenda m’ngalande yaitali, yakuda. Anamva ngati kuti anali olekana ndi matupi awo, akumayandama m’mwamba. Anamva ngati kuti anali kukokeka mofulumira m’ngalandemo kulinga ku malo oŵala kwambiri, ndipo kumapeto kwa ngalandeyo, anaona ziŵalo za banja zimene zinafa kale. Potsirizira pake, anadzuka ali m’matupi mwawo. Komabe, si onse amene akumanapo ndi iliyonse ya mbali zimenezi.
Kukunenedwa kuti zoonedwa zotero zakhala ndi chiyambukiro chabwino pa amene zinawachitikira. Ngati ndi choncho, zinayenera kuwathandiza kuchotsa mantha awo a imfa ndipo zinayenera kuwapatsa chidaliro chakuti moyo uli ndi tanthauzo. Koma nthaŵi zonse zimenezo sizinakhale choncho. Ambiri amapitirizabe kuwopa imfa ndi kusoŵa chidaliro ponena za kukhalako kwa tanthauzo la moyo.
Awo amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo amanena kuti amapeza m’zoonedwa zoterozo chichirikizo cha lingaliro lakuti moyo wa munthu umabadwanso m’mipangidwe ya moyo yosiyanasiyana. Koma kodi chiphunzitso chimenechi chingakhulupiriridwe? Kodi kubadwanso kwa moyo kumaperekadi mfungulo ya zinsinsi za moyo? Kodi tikhoza kupeza mayankho alionse a mafunso akuti, Kodi munayamba mwakhalako? Kodi mudzakhalakonso? Kodi anthu ali ndi moyo umene umatuluka m’thupi pa imfa? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani zotsatira.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Kubadwanso kwa moyo nkofunika kwambiri m’zipembedzo Zakummaŵa
[Chithunzi patsamba 19]
Gudumu la moyo la Ahindu