Kodi Mumakhulupirira Kuti Munthu Akafa Amabadwanso M’moyo Wina?
“KODI ukumkumbukira mtsikana uja timakhala naye pafupi kuno ku India amene unali kukondana naye paubwana wako?” Mukundbhai analembera mwana wake wamwamuna, wophunzira payunivesite ku United States. “Kwangotsala milungu ingapo kuti akwatiwe. Ndati mwina ungafune kudziŵa.”
Nchifukwa ninji bamboyu anauza mwana wake nkhaniyo? Ndi iko komwe, Mukundbhai ndiye anathetsa chibwenzi cha paunyamata chimenecho mwaukali zaka zambiri zapitazo. Ndiponso nthaŵiyo, mwana wakeyo anali atakhala zaka zisanu ndi chimodzi ku United States kumaphunziro apamwamba. Sanali kulemberana naye makalata mtsikanayo nthaŵi yonseyo, ndipo Mukundbhai anali kudziŵa zimenezo.
Nanga anaderanji nkhaŵa? Mukundbhai anatero chifukwa anakhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso kwina.a Ngati zingachitike kuti kukondana kwawo paubwana kunali chifukwa chakuti kale anali okwatirana m’moyo wina, ingakhale nkhanza kuwalekanitsa tsopano pamene afika msinkhu umene angakwatirane. Mukundbhai anangofuna kumdziŵitsa mwana wakeyo zimene zinali kuchitika mtsikanayo asanakhale mkazi wa mwamuna wina m’moyo uno.
Nachi chitsanzo china. Mwana wamkazi wazaka zinayi anavutika masiku ambiri m’chipatala ku Mumbai, India. Matenda ake anali akuti mtsempha wina mumtima sumagwira bwino ntchito. Makolo ake achuma sanathe kupirira kuona mwanayo akuvutika. Koma iwo anati: “Tiyenera kulandira zimenezi. Mwina pali zimene anachita m’moyo wake wina kuti izi zimchitikire.”
Chikhulupiriro chakuti munthu akafa amabadwanso kwina nchamphamvu kwambiri pamoyo wa Ahindu, Abuda, Ajaini, Asiki, ndi anthu a zipembedzo zina za ku India. Zochitika m’moyo—kukondana kwa mnyamata ndi mtsikana ndi mavuto aakulu omwe—amati ndi zotsatira zake za ntchito za munthu pamene anali m’moyo wina.
Anthu ambiri m’maiko a Kumadzulo akopekanso ndi chiphunzitso chakuti munthu akafa amabadwanso kwina. Shirley MacLaine, woseŵera m’mafilimu ku America, amatero kuti iyeyo amakhulupirira zimenezo. Mlembi Laurel Phelan wa ku Vancouver, British Columbia, Canada, amati amakumbukira zinthu za m’miyoyo 50 yosiyanasiyana yakumbuyo imene anabadwamo. Mu 1994 kufufuza kofunsa anthu malingaliro awo kumene a CNN/USA Today anachita kunasonyeza kuti anthu achikulire oposa 270 mwa 1,016 anatero kuti amakhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso kwina. Ngakhale a gulu la New Age amakhulupiriranso kuti munthu akafa amabadwanso kwina. Koma kodi ndi umboni wotani umene umachirikiza chikhulupiriro chimenechi?
“Kukumbukira zinthu za m’moyo wapitapo!” amatero okhulupirira kuti munthu akafa amabadwanso kwina. Chotero, pamene Ratana wazaka zitatu ku Bangkok anayamba “kukumbukira za moyo wake wapitapo pamene anali mkazi wopembedza yemwe anafa ali ndi zaka za ku ma 60,” omvetsera ochuluka anavomereza kuti zimenezo zinali umboni wakuti munthu akafa amabadwanso kwina.
Komabe, ambiri amakayika. Ndiponso zitheka kufotokozera mwina zochititsa anthu kuganiza kuti akukumbukira za moyo wapitapo.b M’buku lake lakuti Hinduism: Its Meaning for the Liberation of the Spirit, Mhindu wafilosofi Nikhilananda akutero kuti ‘maganizo a munthu sangatsimikize kuti atafa panachitika zakuti ayi.’ Koma iye akunenetsabe kuti “chiphunzitso cha kubadwanso nchotheka kwambiri.”
Koma kodi Baibulo limachirikiza chiphunzitso chimenechi? Ndipo kodi Mawu a Mulungu ouziridwawo amapereka chiyembekezo chotani ponena za akufa?
[Mawu a M’munsi]
a The New Encyclopædia Britannica imanena kuti, “kubadwanso m’moyo wina” kumatanthauza kuti “mzimu wa munthu umabadwanso m’moyo umodzi kapena yambiri yotsatizana, monga munthu, nyama, ngakhale chomera nthaŵi zina.” Liwulo “kubadwanso m’moyo wina” limagwiranso ntchito kufotokoza zimenezi, koma ambiri amangoti “munthu akafa amabadwanso kwina.” Madikishonale ambiri m’zinenero za ku India amagwiritsira ntchito mawu onse aŵiriwo.
[Zithunzi patsamba 4]
Kodi iyeyu akulangidwa chifukwa anachimwa m’moyo wapapitapo?