Ndandanda ya Mlungu wa November 11
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 11
Nyimbo Na. 60 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 3 ndime 7 mpaka 12 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Aheberi 1-8 (Mph. 10)
Na. 1: Aheberi 4:1-16 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Tili Ndi “Nzeru Yochokera Kumwamba”?—Yak. 3:17, 18 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Chofunikira kwa Akhristu Ndi Kukonda Anzawo Basi?—rs tsa. 88 ndime 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph 10: Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2013, tsamba 8 ndi 9.
Mph. 10: Kodi Tingatani Kuti Tisamachite Mantha Tikamalalikira? Nkhani yokambirana pogwiritsira ntchito mafunso awa: (1) Kodi pemphero lingatithandize bwanji ngati timachita mantha tikamalalikira? (2) N’chifukwa chiyani kukonzekera n’kothandiza kuti tisamachite mantha tikakhala mu utumiki? (3) N’chiyani chingatithandize kuti tisamachite mantha tikamalalikira ndi woyang’anira dera? (4) Kodi kuchita mantha kungatilepheretse bwanji kuchita zambiri mu utumiki? (5) Kodi n’chiyani chakuthandizani kuthetsa mantha mu utumiki?
Mph. 10: “Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Hoseya.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 113 ndi Pemphero