Ndandanda ya Mlungu wa December 2
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 2
Nyimbo Na. 61 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 4 ndime 9-14 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Petulo 1 mpaka 2 Petulo 3 (Mph. 10)
Na. 1: 1 Petulo 2:18 mpaka 3:1-7 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chipembedzo Choona Chimaphunzitsa Zimene Baibulo Limanena Komanso Chimadziwitsa Anthu Dzina la Mulungu—rs tsa. 89 ndime 3-4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Timakhulupirira Kuti Yesu Ndi Mesiya?—Luka 24:44; Agal. 4:4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani. Limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo Loweruka loyambirira la mwezi wa December. Pogwiritsa ntchito tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya December, sonyezani mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo.
Mph. 15: Kodi Mwaiyesa? Nkhani yokambirana. Kambani nkhani yofotokoza mfundo zachidule za m’nkhani zotsatirazi zomwe zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu waposachedwapa. Nkhani zake ndi zakuti: “Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwa Kuti Izithandiza Ifeyo Komanso Anthu Ena” (km 12/12), “Muzigwiritsira Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa” ndi yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Angakonde Magazini Awa?” (km 5/13). Pemphani omvera kuti afotokoze mmene kugwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’nkhanizi kwawathandizira.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 12 ndi Pemphero