Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/13 tsamba 2
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 12/13 tsamba 2

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ngati talowa mu utumiki ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzathu, kapena ngati tapeza munthu panyumba amenenso si mwamuna kapena mkazi mnzathu?

Ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene anthu ambiri satsatira mfundo za makhalidwe abwino, timayembekezera kuti abale ndi alongo athu azitsatira kwambiri mfundo zimenezi. Ngakhale titakhala kuti tilibe cholinga chilichonse choipa, nthawi zonse tifunika kupewa kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse ena kapena zimene zingatipangitse kuchita zinthu zolakwika. Zimenezi zikusonyeza kuti tifunikanso kukhala osamala tikakhala mu utumiki.

Tikakhala mu utumiki, nthawi zambiri timakumana ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzathu, amene amaonetsa ngati ali ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Ngati tili tokha, ndipo tafika panyumba inayake n’kupeza munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzathu, zingakhale bwino kumulalikira tili panja m’malo molowa m’nyumba. Ngati munthuyo wasonyeza chidwi, mungakonze zodzabweranso muli ndi munthu wina kapena pa nthawi imene anthu ena a pakhomopo adzakhale ali panyumba. Ngati zimenezi sizingatheke, ndi bwino kupempha wofalitsa wina, wamkazi kapena wamwamuna kuti adzapiteko. Mfundo imeneyi ingagwirenso ntchito ngati tili ndi phunziro lomwe si mwamuna kapena mkazi mnzathu.—Mat. 10:16.

Tifunikanso kukhala osamala tikamasankha munthu woti tiyende naye mu utumiki wakumunda. Ngakhale kuti nthawi zina n’zotheka kuti m’bale ndi mlongo amene si okwatirana ayendere limodzi mu utumiki, zingakhale bwino kuchita zimenezi ngati mukulalikira ndi gulu. Nthawi zambiri, ngakhale pamene tili mu utumiki, si bwino kukhala nthawi yaitali tili tokhatokha ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzathu, yemwenso sitili naye pa banja. Choncho, m’bale amene akutsogolera msonkhano wokonzekera utumiki ayenera kukhala wosamala akamagawa anthu oti ayendere limodzi mu utumiki, makamaka achinyamata.

Ngati titamachita zinthu moyenera, tingapewe ‘kuchita chilichonse chokhumudwitsa’ eni akefe kapenanso anthu ena.—2 Akor. 6:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena