Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! May ndi June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena gawirani timapepala totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani? kapena kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? July: Gawirani timabuku totsatirati: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu ndi kakuti, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha.
◼ Baibulo la Dziko la Tsopano Lachikuto Chofewa: Mabaibulo amenewa amachokera ku Japan, choncho azibwera pang’onopang’ono mpaka aliyense adzalandire. Komanso dziwani kuti nthambi ya South Africa idzalandira Mabaibulo enanso a mtunduwu mu October chaka chino. Zimenezi zikutanthauza kuti mipingo idzalandira Mabaibulo amenewa mu December.