Ndandanda ya Mlungu wa June 30
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 30
Nyimbo Na. 51 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 8-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 14-16 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “M’pofunika Kumapitako Mwachangu.” Nkhani. Mukamaliza kukamba nkhaniyi, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayambitsire maphunziro Loweruka loyamba la mwezi wa July pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 8.
Mph. 20: “Kuphunzira Patokha N’kothandiza Kwambiri.” Onani tsamba 3-4. Nkhani yokambirana. Funsani wofalitsa amene amakonda kuphunzira payekha.
Nyimbo Na. 69 ndi Pemphero