Ndandanda ya Mlungu wa August 4
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 4
Nyimbo Na. 109 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 14-19 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 4-6 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 4:17-33 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Baibulo Limati Ena Sadzapulumutsidwa Konse—rs tsa. 95 ndime 3–tsa. 96 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Yehova Amaweruza Anthu Amene Amanamizira Ena Milandu—lv tsa. 137 ndime 11-12 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a August. Nkhani yokambirana. Pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magaziniwa kumapeto kwa mlungu limodzi ndi kapepala. Kenako funsani omvera mafunso awa: N’chifukwa chiyani tiyenera kugawiranso magazini kumapeto kwa mlungu ngati pakufunika kutero? Kodi ndi nthawi iti pamene tingachite zimenezi?
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero