Ndandanda ya Mlungu wa August 18
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 18
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 1-6 ndi bokosi patsamba 184 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 10-13 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 10:1-16 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chake Chikhulupiriro Chiyenera Kukhala ndi Ntchito—rs tsa. 97 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Dina Ndi Chitsanzo Chotichenjeza—lv tsa. 102-103 ndime 13-15 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: “Patha Zaka 100 Tikulengeza za Ufumu.”—Gawo 1. Nkhani yokambirana. Kambiranani ndime 1 mpaka 3. Mukakambirana funso la ndime 3, funsani ofalitsa awiri omwe akhala Mboni kwa nthawi yaitali. Apempheni kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene zinawachitikira atangoyamba kumene kulalikira.
Mph. 15: “Patha Zaka 100 Tikulengeza za Ufumu.”—Gawo 2. Mafunso ndi mayankho. Kambiranani ndime 4 mpaka 6. Mukamakambirana ndime 5, funsani apainiya okhazikika awiri kuti afotokoze zimene anachita kuti akwanitse kuyamba upainiya.
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero