Ndandanda ya Mlungu wa September 1
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 1
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 13-20 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 17-21 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 17:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Satana Si Maganizo Oipa Chabe Amene Anthu Angakhale Nawo—rs tsa. 353 ndime 2-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndani Ali M’manda Achikumbutso?—bh tsa. 72-73 ndime 16-20 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a September. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene zinachitika pogwiritsa ntchito zimene tinaphunzira m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tiziuza Anthu Zokhudza Ufumu Molimba Mtima.” Pemphani omvera kuti anene mavuto amene amakumana nawo akamalalikira za Ufumu. Nanga amathana nawo bwanji?
Mph. 10: Zimene Zinachitika Pogawira Kapepala Kapadera. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pogwiritsa ntchito nkhani zomwe zili mu Utumiki wa Ufumu uno, fotokozani mwachidule kufunika koti tipitirize kulengeza za Ufumu. Kodi mpingo unachita zotani pogwiritsa ntchito malangizo amenewa? Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene zinachitika pogawira kapepala kapaderaka?
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero