Ndandanda ya Mlungu wa September 15
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 15
Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 1 ndime 10-17 ndi bokosi patsamba 14 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 26–29 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 27:15-23 ndi 28:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Mulungu Sanalenge Mdyerekezi—rs tsa. 354 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kuopsa kwa Tchimo—bh tsa. 63 ndime 13-14 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita mu utumiki m’chaka chautumiki chathachi komanso zimene unachita pa nthawi ya ntchito yapadera mu August. Tchulani zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo yamikirani abale ndi alongo chifukwa cha zimenezi. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo m’mwezi wa August. Komanso funsani wofalitsa amene anawonjezera zochita mu utumiki pa nthawiyi. Pomaliza, tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kuyesetsa kuti uchite bwino chaka cha utumiki talowachi. Komanso fotokozani zimene zingathandize mpingo wanuwo kuti mukwanitse kuchita zimenezi.
Mph. 15: “Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Nahumu.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 46 ndi Pemphero