Ndandanda ya Mlungu wa September 29
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 29
Nyimbo Na. 106 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 2 ndime 1-11 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 33-36 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 33:24-49 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Musaderere Mphamvu ya Mdyerekezi—rs tsa. 355 ndime 2–tsa. 356 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Khalani Osamala Munthu Wina Akakufunsani Chifukwa Chake Mumakhulupirira Zinthu Zinazake—bh tsa. 160 ndime 13-15 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo cha mmene tingayambitsire maphunziro a Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa October pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 4. Limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 4:13 ndi 2 Akorinto 4:1, 7. Kenako kambiranani mmene mavesiwa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 10: Funsani Wogwirizanitsa Ntchito za Bungwe la Akulu. Kodi mumagwira ntchito zotani? Kodi mumaganizira zinthu ziti mukamagawa nkhani za Msonkhano wa Utumiki? N’chifukwa chiyani wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu sayenera kuonedwa ngati ndiye wamkulu pa akulu onse komanso mpingo wonse?
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero