Ndandanda ya Mlungu wa February 2
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 2
Nyimbo Na. 134 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 8 ndime 1-8 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 8-10 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 8:13-27 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Thandizani Anthu Kumvetsa Mawu a Mulungu—bt tsa. 57-58 ndime 14-16 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tikuphunzira Chiyani kwa Ophunzira a Yesu Oyambirira?—Mat. 4:18-22 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
MUTU WA MWEZI UNO: ‘Tumikirani Ambuye Monga Kapolo Modzichepetsa Kwambiri.’—Mac. 20:19.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu February. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo chosonyeza zimene tinganene pogawira magaziniwa pogwiritsa ntchito zitsanzo zaulaliki zomwe zili pa tsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto.
Mph. 10: Zofunika pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira ndi mfundo zomwe zili mu nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tingatani Ngati Tapeza Munthu Waukali?” Kenako apempheni kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo.
Nyimbo yatsopano yakuti: “Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima” ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo nyimboyi. Ngati simungathe kuchita dawunilodi nyimboyi pa webusaiti yathu, mungaimbe nyimbo nambala 46.