N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”?
Kodi ndinu wodzipereka pa ntchito zabwino? Popeza timalalikira za Ufumu, tiyeneradi kukhala odzipereka. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tikambirane lemba la Tito 2:11-14.
Vesi 11: Kodi ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu’ n’chiyani? Nanga timapindula bwanji ndi kukoma mtima kumeneku?—Aroma 3:23, 24.
Vesi 12: Kodi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kwatiphunzitsa chiyani?
Vesi 13 ndi 14: Popeza tayeretsedwa, kodi tili ndi chiyembekezo chotani? Nanga chifukwa chachikulu chimene Mulungu watiyeretsera m’dziko losaopa Mulunguli n’chiyani?
Kodi mavesiwa akuthandizani bwanji kukhala odzipereka pa ntchito zabwino?