Ndandanda ya Mlungu wa May 4
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 4
Nyimbo Na. 46 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 12 ndime 9-15 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 1-3 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Samueli 2:24-32 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Tsanzirani Paulo Poteteza Choonadi—bt tsa. 87-88 ndime 6-8 (Mph. 5)
Na. 3: Malonjezo a M’Baibulo Akwaniritsidwa Posachedwapa—igw tsa. 16 ndime 4–tsa. 17 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aef. 5:15, 16.
Mph. 10: Zofunika pampingo. Mungachitenso chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini atsopano.
Mph. 5: Mabuku Ogawira M’mwezi wa May ndi June. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’buku kapena m’kapepalako. Kenako chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire buku kapena kapepalako.
Mph. 15: Tizigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yathu Polalikira M’dera Limene Sililalikidwa Kawirikawiri. Nkhani yokambirana. Ngati n’zotheka, ikambidwe ndi mkulu amene analalikirapo m’dera lomwe sililalikidwa kawirikawiri. Funsani wofalitsa amene analalikirapo m’dera lomwe sililalikidwa kawirikawiri. Kodi kuchita zimenezi kunamuthandiza bwanji iyeyo ndi banja lake? Nanga kunamuthandiza bwanji kuti azilalikira mwaluso komanso kuti alimbitse ubwenzi wake ndi Yehova? Kodi anatani kuti akwanitse kulalikira kudera limeneli? Fotokozani kuti akulu ndi okonzeka kuthandiza aliyense amene akufuna kulalikira kudera lomwe sililalikidwa kawirikawiri. Thandizani omvera kudziwa kuti kulalikira m’madera omwe salalikidwa kawirikawiri ndi njira yabwino yogwiritsa ntchito nthawi yathu.
Nyimbo yatsopano ya mutu wakuti, “Athandizeni Kukhala Olimba” ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo nyimboyi. Ngati simungathe kuchita dawunilodi nyimboyi pa webusaiti yathu, mungaimbe nyimbo nambala 44.