Ndandanda ya Mlungu wa May 25
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 25
Nyimbo Na. 9 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 13 ndime 11-18 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 13-15 (8 min.)
Na. 1: 2 Samueli 13:34–14:7 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Tizikhulupirira Bungwe Lolamulira—bt tsa. 111 ndime 9-10 (5 min.)
Na. 3: Mzimu Woyera Umatithandiza Kuchita Zambiri—Eks. 35:30-35 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Muzithandiza anthu onse kudziwa choonadi molondola.—1 Tim. 2:3, 4.
10 min: Funsani Woyang’anira Kagulu ka Utumiki Wakumunda. Funsani m’bale amene amayang’anira kagulu ka utumiki mafunso otsatirawa: Kodi ntchito yanu ndi yotani? Kodi mumakwanitsa bwanji kuchita maulendo a ubusa kwa anthu amene ali m’kagulu kanu? N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti wofalitsa aliyense azikudziwitsani akasamuka kapena akasintha nambala yake ya foni? N’chifukwa chiyani akulu amakonza zoti ofalitsa azikumana m’timagulu tawo pokonzekera utumiki, m’malo mongopangira pamodzi?
20 min: “Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova.” Mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero