Ndandanda ya Mlungu wa July 13
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 13
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 15 ndime 20-23 ndi bokosi patsamba 157 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 9-11 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 9:24-28 ndi 10:1-3 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Baibulo Lingakuthandizeni Kuchepetsa Nkhawa—igw tsa. 24 ndime 4–tsa. 25 ndime 2 (5 min.)
Na. 3: Mawu a Mulungu Amakwaniritsidwa Nthawi Zonse—Yes. 46:9-10; Yoh. 17:17 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Pitani mukaphunzitse anthu kuti akhale ophunzira anga.’—Mat. 28:19, 20.
10 min: Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga. Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. Mutenge mfundo zina m’buku lakuti, ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga,’ tsamba 87 mpaka 89. Pomaliza, tchulani nkhani zina zomwe tiphunzire mwezi uno pa Msonkhano wa Utumiki, ndipo kambiranani mmene nkhanizi zikugwirizanirana ndi mutu wa mwezi uno.
10 min: Anayesetsa Kuyambitsa Phunziro la Baibulo. Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2015, tsamba 55 ndime 1 mpaka tsamba 56 ndime 1. Komanso tsamba 69 ndime 2 mpaka tsamba 70 ndime 1. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
10 min: “Tiziyesetsa Kuthandiza Anthu Kuti Akhale Ophunzira a Yesu.” Mafunso ndi mayankho. Funsani mwachidule wofalitsa mmodzi kapena awiri amene ndi aluso poyambitsa komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Kodi amamva bwanji akathandiza munthu kuphunzira choonadi n’kuyamba kutumikira Yehova?
Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero