Ndandanda ya Mlungu wa July 20
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 20
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 16 ndime 1-9 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 12-14 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 12:21-30 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Yehova Amadalitsa Anthu Omutumikira ndi Mtima Wonse—dp tsa. 7-8 ndime 7-11 (5 min.)
Na. 3: Kodi Baibulo Lingathandize Bwanji Amuna M’banja?—igw tsa. 26 ndime 1-2 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Pitani mukaphunzitse anthu kuti akhale ophunzira anga.’—Mat. 28:19, 20.
20 min: “Zithunzi Zofotokoza Nkhani ya M’Baibulo.” Nkhani yokambirana yomwe ili patsamba 3 mpaka 6. (Pitani pa jw.org/ny kuti mupange dawunilodi Utumiki Wathu wa Ufumu wa July womwe uli ndi zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo.) Ngati n’zotheka, sankhiranitu ana oti adzawerenge mawu a anthu a m’nkhaniyi ali pamalo awo. Kenako, pemphani ana angapo kuti abwere kupulatifomu kuti adzakambirane mafunso omwe ali m’bokosi lakuti, “Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Nkhaniyi?” Muyenera kupempheratu chilolezo kwa makolo a anawo. Pomaliza limbikitsani makolo kuti azigwiritsa ntchito mabuku kapena mavidiyo a ana pothandiza ana awo kukhala ophunzira a Yesu.
10 min: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambirana.
Nyimbo Na. 66 ndi Pemphero