Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Atumiki a Yehova amachita zambiri pa nyengo ya Chikumbutso. Kutatsala miyezi 5 kuti Chikumbutso cha chaka cha 2015 chichitike, panali apainiya othandiza okwana 2,829. Koma m’miyezi ya March, April ndi May, chiwerengerochi chinakwera kufika pa 4,302. Tinachititsa maphunziro a Baibulo 140,403 m’mwezi wa March. Kunena zoona, Yehova anatamandika kwambiri pa miyezi itatu imeneyi. Tiyeni tipitirize kuchita zambiri mu ntchito ya Ambuye podziwa kuti zonse zimene tikuchita sizidzapita pachabe.—1 Akor. 15:58.