Ndandanda ya Mlungu wa December 7
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 7
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 22 ndime 18-22 ndi bokosi patsamba 228 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 10-14 (8 min.)
Na. 1: 2 Mbiri 13:13-22 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Munthu Angasiye Bwanji Kuseweretsa Maliseche?—lv tsa. 218-219 (5 min.)
Na. 3: Kodi Mawu Oti “Kaisara” Amanena za Ndani?—lv tsa. 44-45 ndime 18-21 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezu Uno: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”—Mac. 14:22.
10 min: “Tiyenera Kukumana ndi Masautso Ambiri Kuti Tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.” Nkhani yochokera pamutu wa mwezi uno. Werengani ndi kukambirana Machitidwe 14:21, 22 ndi 1 Petulo 4:12-14. (Onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 2014, tsamba 13, ndime 3-6.) Tchulani nkhani zina zomwe tiphunzire mwezi uno pa Msonkhano wa Utumiki ndipo kambiranani kugwirizana kwake ndi mutu wa mwezi uno. Limbikitsani aliyense kuti ngati angakwanitse akaonere vidiyo yakuti ‘Yendani mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Zooneka ndi Maso’ pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamawa. Ngati simungakwanitse kuonera vidiyoyi pezani nkhani ina yoti mukambe m’malo mwa vidiyoyi.
10 min: Kodi Tingayankhe Bwanji? (Akol. 4:6) Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 69, ndime 1-3. Chitani zitsanzo ziwiri. M’chitsanzo choyamba, mwininyumba akulankhula mwachipongwe ndipo wofalitsa akumuyankha nthawi yomweyo mwaukali ndipo zinthu sizikutha bwino. M’chitsanzo chachiwiri, wofalitsa akuganiza kaye kenako n’kuyankha modekha ndipo zotsatira zake n’zabwino.
10 min: “Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Habakuku.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 74 ndi Pemphero