Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Habakuku
1. N’chiyani chingatichititse kumva ngati mneneri Habakuku?
1 Tikamaona zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli, timamva ngati mmene mneneri Habakuku anamvera. Iye anafunsa Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa?” (Hab. 1:3; 2 Tim. 3:1, 13) Kuganizira uthenga wa Habakuku komanso chitsanzo chake chokhala wokhulupirika, n’kolimbikitsa kwambiri pamene tikuyembekezera tsiku lachiweruzo la Yehova.—2 Pet. 3:7.
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro?
2 Tizikhala ndi Chikhulupiriro: Habakuku sanafooke chifukwa cha zinthu zimene zinkachitika pa nthawiyo, koma anapitirizabe kukhala tcheru potumikira Mulungu. (Hab. 2:1) Yehova anamutsimikizira kuti mawu amene anamuuza, adzakwaniritsidwa pa nthawi yoyenera ndiponso kuti “wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Hab. 2:2-4) Kodi ifeyo tingaphunzirepo chiyani pa mawu amenewa? M’malo momangoganizira kuti kodi mapeto abwera liti, ndi bwino kukhulupirira kuti mapetowo adzafikadi. Chikhulupiriro chingatithandize kukhala atcheru komanso kuona kuti utumiki ndi wofunika kwambiri.—Aheb. 10:38, 39.
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osangalala potumikira Yehova?
3 Tizitumikira Yehova Mosangalala: Gogi wa ku Magogi akadzatiukira, chikhulupiriro chathu chidzayesedwa. (Ezek. 38:2, 10-12) Kumbukirani kuti nkhondo imabweretsa mavuto ambiri ngakhale kwa anthu amene apambana nkhondoyo. Mwachitsanzo, chakudya chimasowa, katundu amaonongeka komanso zinthu siziyenda bwino. Kodi ifeyo tidzatani tikadzakumana ndi mavuto ngati amenewa? Habakuku ankadziwa kuti adzakumana ndi mavuto koma anatsimikiza mtima kuti adzakhalabe wosangalala potumikira Yehova. (Hab. 3:16-19) Nafenso, “chimwemwe chimene Yehova amapereka,” chidzatithandiza kupirira mayesero amene akubwerawo.—Neh. 8:10; Aheb. 12:2.
4. Kodi ndi madalitso ati amene tidzapeze, nanga panopa tiyenera kuchita chiyani?
4 Yehova adzapitiriza kuphunzitsa anthu amene adzapulumuke pa chiweruzo chimene chikubwerachi. (Hab. 2:14) Anthu oukitsidwa adzaphunzitsidwanso za Yehova. Choncho tiyeni panopa tizigwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ungapezeke kuti tiuze anthu ntchito zodabwitsa za Yehova.—Sal. 34:1; 71:17.