Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/15 tsamba 3
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 12/15 tsamba 3

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Tidzakambirana mafunso otsatirawa pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 28, 2015. Talemba deti limene tidzakambirane mfundoyi n’cholinga choti aliyense azipezeratu mayankho ake pa nthawi imene tikuchita sukuluyi mlungu uliwonse.

  1. Kodi Davide ankachitira nkhanza anthu omwe anawagwira ku nkhondo, monga mmene ena amaganizira akawerenga pa 1 Mbiri 20:3? [Nov. 2, w05 2/15 tsa. 27]

  2. N’chifukwa chiyani Davide anasonyeza mtima wowolowa manja, nanga n’chiyani chingatithandize kuchitanso zimenezi? (1 Mbiri 22:5) [Nov. 9, w05 10/1 tsa. 11 ndime 7]

  3. Kodi Davide ankatanthauza chiyani pamene anauza Solomo kuti: “Dziwa Mulungu wa bambo wako”? (1 Mbiri 28:9) [Nov. 16, w10 11/1 tsa. 25 ndime 3, 7]

  4. Kodi zimene Solomo anapempha pa 2 Mbiri 1:10 zinasonyeza chiyani, nanga kuganizira zimene timanena m’mapemphero athu kungatithandize bwanji? (2 Mbiri 1:11,12) [Nov. 23, w05 12/1 tsa. 19 ndime 6]

  5. Kodi Yehova amadziwa chiyani mogwirizana ndi lemba la 2 Mbiri 6:29, 30, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera mochokera pansi pa mtima? (Sal. 55:22) [Nov. 30, w10 12/1 tsa. 11 ndime 7]

  6. N’chifukwa chiyani Asa anapemphera kwa Yehova pamene ankafuna kumenyana ndi gulu lalikulu la asilikali, ndipo zimenezi zingatiphunzitse chiyani? (2 Mbiri 14:11) [Dec. 7, w12 8/15 tsa. 8 ndime 6–tsa. 9 ndime 1]

  7. Kodi zimene Yehova anachita ndi Mfumu Yehosafati zimasonyeza chiyani, ndipo zimenezi zingatithandize bwanji anzathu akatilakwira? (2 Mbiri 19:3) [Dec. 14, w03 7/1 tsa. 17 ndime 13; cl tsa. 244 ndime 12]

  8. Kodi masiku ano tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ‘m’malo athu’ ndiponso ‘kuima chilili,’ ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? (2 Mbiri 20:17) [Dec. 21, w05 12/1 tsa. 21 ndime 3; w03 6/1 tsa. 21 ndime 15-16]

  9. Lemba la 2 Mbiri 21:20 limanena zimene zinachitika Yehoramu atafa. Kodi tingaphunzire chiyani palembali? [Dec. 21, w98 11/15 tsa. 32 ndime 4]

  10. Mogwirizana ndi 2 Mbiri 26:5, kodi ndani anathandiza Uziya pamene anali mnyamata, ndipo kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Akhristu olimba? [Dec. 28, w07 12/15 tsa. 10 ndime 2, 4]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena