Ndandanda ya Mlungu wa December 28
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 28
Nyimbo Na. 1 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 23 ndime 19-23 ndi bokosi patsamba 239 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 25-28 (8 min.)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (20 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezu Uno: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”—Mac. 14:22.
15 min: Tizipempherera Abale Athu. Nkhani yokambirana. Poyamba werengani Machitidwe 12:1-11. Ndiyeno kambiranani mfundo zothandiza zimene zili m’buku lakuti Kuchitira Umboni, tsamba 77-80, ndime 5-12. Kenako kambiranani nkhani zatsopano zimene zili pa webusaiti yathu pamene alemba kuti “Malo a Nkhani” kapena onani m’mabuku athu atsopano. Limbikitsani onse kuti azipempherera abale ndi alongo athu amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana ndipo ngati n’kotheka akhoza kumatchula mayina awo m’pemphero.—2 Akor. 1:11; 1 Tim. 2:1, 2.
15 min: Zofunika pampingo.
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero